2 Am. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maganizo ankhanza a Nikanore

1Nikanore atamva kuti Yudasi ndi anthu ake ali m'dera la ku Samariya, adakonzeka kuti akachite nawo nkhondo pa tsiku la Sabata, kuti iyeyo asakapeze zovuta.

2Ayuda amene iye adaaŵaumiriza kumtsata, adamuuza kuti, “Musachite zankhalwe ndi zankhanza zotere, inu mulemekeze tsiku limene Mulungu woonazonse adalilemekeza ndi kulisandutsa loyera koposa masiku ena.”

3Koma Nikanore woipitsitsa uja adafunsa kuti, “Kodi kuli mfumunso kumwamba imene idalamula zolemekeza tsiku la Sabata?”

4Iwo adamuyankha kuti, “Inde, ndi Ambuye amoyo, Mfumu yakumwamba, amene adalamula kuti tizilemekeza tsiku lachisanu ndi chiŵiri.”

5Koma Nikanore adati, “Inensotu ndine mfumu pansi pano, tsono ndikukulamulani kuti mutenge zida zanu, mukachite zimene mfumu yakutumani.” Komabe zimene ankafunazo, sadathe kuzichita.

Yudasi akonzekera nkhondo

6Tsono popeza kuti Nikanore anali wonyada ndi wodzikuza zedi, adatsimikiza zodzamanga chikumbutso cha kugonjetsa Yudasi ndi anthu ake.

7Koma Makabeo sadaleke kukhulupirira mosakaika konse kuti adzalandira thandizo kuchokera kwa Ambuye.

8Adalangiza anthu ake kuti asaope nkhondo ya akunja, koma akumbukire thandizo limene linkachokera kumwamba kuyambira kale lomwe. Adaŵauzanso kuti tsopano ayembekeze kuti Wamphamvuzonse adzaŵapambanitsanso.

9Adaŵalimbitsa mtima poŵauza mau a Malamulo ndi a aneneri, naŵakumbutsa za nkhondo zimene adaapambana. Potero adautsa changu chachikulu m'mitima mwao.

10Ataŵalimbitsa mtima motero, adaŵapatsa malamulo ake, naŵafotokozera kuipa kwa akunjawo, amene adaphwanya zimene adalumbira.

11Adaŵapatsa zofunikira pomenya nkhondo, osati zishango zokha kapena mikondo, koma makamaka mau ndi malangizo abwino. Kenaka adaŵafotokozera zimene adaaziwona m'masomphenya, zoyenera kuzikhulupirira.

12Zimene adaaziwonazo ndi izi: Adaaona Oniyasi amene, mkulu wa ansembe onse uja, akupemphera, atatambalitsa manja ake pa fuko lonse la Ayuda. Oniyasiyo anali munthu wabwino ndi waulemu, munthu wosadzikuza ndi wodekha, wolankhula mau bwino, amene adaazoloŵera kukhala ndi makhalidwe ofatsa kuyambira ubwana wake.

13Pambuyo pake munthu winanso adamuwonekera Yudasi. Munthuyo anali ndi imvi, anali waulemu ndi wa ulemerero wodabwitsa.

14Tsono Oniyasiyo adanena kuti, “Ameneyu ndi bwenzi la abale athu, ndipo amapempherera kwambiri fuko lonse ndi mzinda wonse woyera. Ameneyu ndi Yeremiya, mneneri wa Mulungu.”

15Apo Yeremiya adatambasula dzanja lake, nkupatsa Yudasi lupanga lagolide nati,

16“Kwaya lupanga loyerali, imeneyi ndi mphatso ya Mulungu, yomwe udzagonjetsera adani ako.”

17Atamva mau okoma a Yudasi, onse adalimba mtima chifukwa mauwo adautsa mphamvu zao, adalimbitsa chamuna m'mitima mwa anyamatawo. Tsono Ayudawo adapangana zoti asabindikirenso m'zithando koma athamangire adani, ndi kukamenyana nawo cholimbana ndi manja, kuti nkhondo itheretu mwamsanga. Adaaganiza zimenezo popeza kuti mzindawo ndi Nyumba ya Mulungu yomwe, zonsezo zinali pa zoopsa.

18Sankadera nkhaŵa kwambiri akazi ao, ana ao, anansi ao kapena abale ao, koma makamaka ankadera nkhaŵa Nyumba yoyera ya Mulungu.

19Nawonso oyenera kutsalira mumzinda ankavutika mu mtima, poganizira za m'mene zidzayendere pa nkhondo yomenyana pa mtetete.

Kugonja ndi kufa kwa Nikanore

20Nthaŵi yonseyo onse ankadikira kuti aone m'mene idzathere nkhondoyo. Adani anali atasonkhana ndi kufika kufupi, ankhondo ao atandanda pa mizere yankhondo, njovu atazikhazika pa malo oyenera, anthu okwera pa akavalo atakhala m'mphepetemu.

21Makabeo poona unyinji wa anthu obwera kwa iye, ataonanso zida zao za mitundu yosiyanasiyana, ndiponso ukali wa njovu zaozo, adakweza manja kumwamba. Adayamba kupemphera kwa Ambuye amene amachita zozizwitsa, chifukwa adaadziŵadi kuti Ambuyewo sayang'ana mphamvu ya zida, koma amapambanitsa oyenera kupambana, monga momwe Iye mwini akufunira

222Maf. 19.35Tsono adapempha Mulungu kuti, “Inu Ambuye, mudaatuma mngelo wanu pa nthaŵi ya Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, iye nkupha ankhondo a Senakeribu okwanira 185,000.

23Inu mwiniwake wa dziko lakumwamba, mutumenso mngelo wanu wabwino tsopano lino, kuti aŵachititse mantha ndi kuŵadetsa nkhaŵa adani athuŵa.

24Anthu olalatira dzina lanu aja, amene akufuna kumenyana ndi mpingo wanu wopatulika, muŵaonongeretu ndi mphamvu zanu zazikulu.” Adalitsiriza motero pemphero lake.

25 1Am. 7.43-50 Nikanore adafika ndi gulu lake, akuliza malipenga ndi kumaimba nyimbo zankhondo.

26Koma Yudasi ndi anthu ake adayamba kumenyana nawo nkhondo, akupempha chithandizo cha Mulungu.

27Motero pamene ankamenya nkhondo ndi zida zam'manja, kwinaku akupemphera chamumtima, adapha anthu opitirira 35,000. Choncho adakondwa kwambiri poona kuti Mulungu waŵathandiza.

28Nkhondoyo itatha, pamene ankabwerera ndi chimwemwe chachikulu, adazindikira Nikanore ali thasa, atafa, zovala zankhondo zili m'thupi.

29Tsono padakhala kufuula ndi kusokosadi, chifukwa onse ankathokoza Ambuye Amphamvuzonse m'chilankhulo cha makolo ao.

30Yudasi, amene adaadzipereka kwathunthu potsogolera nkhondo yopulumutsa abale a m'dziko mwake, osaleka chifundo chomwe ankaŵachitira kuyambira pa unyamata wake, adalamula kuti adule mutu wa Nikanore ndi mkono wake, ndi kubwera nazo ku Yerusalemu.

31Atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa anthu onse a mtundu wake naika ansembe pafupi ndi guwa, nkuitananso onse aja okhala m'chinyumba chankhondo.

32Adaŵaonetsa mutu wa Nikanore ndi mkono wake umene munthu wonyada uja sankaopa kuutambalitsa mwachipongwe kuloza Nyumba ya Mulungu Wamphamvuzonse.

33Kenaka adadula lilime la Nikanore wosamverayo nati, “Ndidzalipereka ku mbalame kuti zidye, ndipo poyang'anana ndi Nyumba ya Mulungu ndidzapachikapo ziwalo zake zimene zidadulidwa chifukwa cha kupenga kwake.”

34Apo onse adatamanda Ambuye akumwamba adati “Ngwodala Mulungu amene adateteza malo ake kuti asaipitsidwe.”

35Pambuyo pake Yudasi adapachika mutu wa Nikanore pamwamba pa chinyumba chankhondo, kuti uwoneke kwa onse ngati umboni wa chithandizo cha Ambuye.

361Am. 7.49Tsono onse adamvana kuti azikumbukira tsikulo. Adapangananso kuti azichita chikondwerero pa tsiku la 13 la mwezi wa 12, wotchedwa Adara m'chilankhulo Chachisiriya. Limeneli linali tsiku lodikira tsiku la Mordekai.

Mau otsiriza a mlembi

37Imeneyi ndiyo mbiri ya Nikanore. Kuyambira nthaŵi imeneyo, mzinda wa Yerusalemu udakhala uli m'manja mwa Ahebri. Nanenso tsono nkhani yangayi ndiilekera pomwepa.

38Ngati zimene ndalembazi nzomveka bwino ndi zakupsa, ai ndimafuna zimenezo kumene. Koma ngati nzosachititsa chidwi ndi zosagwira mtima, khulupirirani kuti ndidaachita chotheka chonse kuti ndilembe bwino.

39Pajatu vinyo amapweteka, kumumwa payekha, madzinso sakoma, kuŵamwa paokha; koma vinyo kumsakaniza ndi madzi amakhala chakumwa chokoma zedi ndi chosangalatsa. Chimodzimodzinso luso lolembera bwino nkhani, limakondweretsa anthu oŵerenga nkhanizo. Ai, ndikafika apo, ndaima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help