Mt. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za miyambo ya makolo a Ayuda(Mk. 7.1-13; Lk. 11.37-41)

1Tsiku lina Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo adadza kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu. Adamufunsa kuti,

2“Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo? Sasamba m'manja moyenera akamadya chakudya.”

3Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu?

4 wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.”

23Koma Yesu sadamuyankhe mau ndi amodzi omwe. Ophunzira ake adadza nampempha kuti, “Muuzeni azipita, onani akubwera natisokosera.”

24Yesu adati, “Inetu Mulungu adandituma kwa amene ali ngati nkhosa zotayika pa mtundu wa Aisraele.”

25Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.”

26Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.”

27Maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amadyako nyenyeswa zimene zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la mbuye ao?”

28Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.

Yesu achiritsa anthu ambiri

29Pambuyo pake Yesu adachoka kumeneko, nayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya. Kenaka adakwera m'phiri nakakhala pansi kumeneko.

30Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa.

31Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele.

Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zinai(Mk. 8.1-10)

32Yesu adaitana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya. Sindifuna kuŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, kuwopa kuti angalefuke pa njira.”

33Ophunzirawo adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa tingaŵapezere kuti chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?”

34Yesu adaŵafunsa kuti, “Kaya buledi muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri, ndiponso tinsomba toŵerengeka.”

35Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi.

36Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja.

37Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nkudzaza madengu asanu ndi aŵiri.

38Koma tsono anthu amene adaadyawo, analipo zikwi zinai amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana.

39Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye adaloŵa m'chombo napita ku dera la Magadani.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help