1Pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ndi gulu lake lonse lankhondo ku Yerusalemu, nazinga mzindawo.
2Pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha ufumu wa Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mweziwo, malinga a mzindawo adabooledwa.
3Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni adaloŵa nakakhala pa chipata chapakati. Anali aŵa: Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, ndi Neregali-Sarezere winanso mkulu wolamulira gulu lankhondo lapatsogolo, pamodzi ndi akuluakulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.
4Pamene Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adaŵaona, iyeyo pamodzi ndi ankhondo ake adathaŵa mumzindamo usiku, kudzera ku munda wa mfumu, kubzola pa chipata cha pakati pa zipupa ziŵiri. Adathaŵira ku Araba.
5Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola ndi kukamgwira Zedekiyayo ku zigwa za ku Yeriko. Mfumuyo ataigwira, adapita nayo kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ku Ribula m'dziko la Hamati. Ndipo adagamula mlandu wake komweko.
6Tsono mfumu ya ku Babiloni idapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribula, iyeyo akuwona. Idaphanso atsogoleri onse a ku Yuda.
7Kenaka idamkolowola maso Zedekiyayo, nimmanga ndi maunyolo nkupita naye ku Babiloni.
8Ababiloni adatentha nyumba yaufumu, Nyumba ya Chauta pamodzi ndi nyumba zina zonse za anthu. Ndipo adagwetsa malinga a Yerusalemu.
9Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo, adatenga anthu onse otsala a mumzindawo kupita nawo ku Babiloni. Ameneŵa ndiwo amene adaadzipereka kwa iye, ndiponso anthu amene adaatsalira.
10Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondoyo, adasiya anthu okhaokha osauka kwambiri, ndi opanda nkanthu komwe m'dziko la Yuda. Ndipo adaŵapatsa minda yamphesa ndi minda inanso.
Amasula Yeremiya m'ndende11Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adatumiza mau kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo, onena za Yeremiya. Adati,
12“Mtenge, umsamale bwino, usamvute, koma umchitire zimene afuna.”
13Motero Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo uja, adanyamuka pamodzi ndi Nebusazibani mtsogoleri wamkulu, Neregali-Sarezere mkulu wolamulira gulu lankhondo linanso ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni.
14Iwowo adakatenga Yeremiya ku bwalo la alonda, nakampereka kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, kuti amumasule ndi kumtumiza kunyumba kwake. Motero Yeremiya adakakhala ndi anthu ake.
Za kupulumuka kwa Ebedemeleki15Chauta adalankhula ndi Yeremiya pamene anali m'ndende ku bwalo la alonda. Adati,
16“Pita ukauze Ebedemeleki Mkusi uja kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akunena kuti, ‘Zidzachitikadi zimene ndidaanena za mzinda uno, ndipo nzoipa osati zabwino, ai. Zidzachitikadi pa nthaŵi yake, iwe ukupenya.
17Iweyo ndidzakupulumutsa tsiku limenelo, ndipo sudzaperekedwa kwa anthu amene umaŵaopa.
18Ndithu ndidzakupulumutsa, ndipo sudzaphedwa pa nkhondo. Udzapulumuka chifukwa choti wandikhulupirira,’ ” akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.