1 2Maf. 15.1-7; 2Mbi. 26.1-23; 2Maf. 15.32-38; 2Mbi. 27.1-9; 2Maf. 16.1-20; 2Mbi. 28.1-27; 2Maf. 18.1—20.21; 2Mbi. 29.1—32.33 Buku lino likufotokoza zinthu zimene Mulungu adaululira Yesaya, mwana wa Amozi, zokhudza Yuda ndi Yerusalemu pa masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda.
Mulungu adzudzula anthu ake2Chauta adati,
“Tamvera, iwe mlengalenga,
tchera khutu, iwe dziko lapansi,
Ine Chauta ndikulankhula.
Ndidabereka ana ndi kuŵalera,
koma andigalukira.
3Ng'ombe imadziŵa mwini wake,
bulu amadziŵa kumene mwini wake amamdyetsera,
koma Aisraele sadziŵa,
anthu anga samvetsa konse.”
4Ha, mtundu wochimwa,
inu anthu olemedwa ndi machimo,
obadwa kwa anthu ochita zoipa,
ana omira m'zoipa!
Mudasiya Chauta,
mudanyoza Woyera uja wa Israele,
mudamufulatira kwathunthu.
5Kodi ndi pati ndingakumenyeninso,
popeza kuti mukupandukirapandukira?
Aliyense mutu wake uli ndi mabala kale,
ndipo mtima wake wafookeratu.
6Kuchokera kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino,
ponse pali mikwingwirima ndi zilonda,
mabala ali magazi chuchuchu.
Mabala ake ngosatsuka, ngosamanga,
ndiponso ngosapaka mafuta ofeŵetsa.
7Dziko lanu lasanduka bwinja,
mizinda yanu aitentha.
Alendo akukuwonongerani dziko inu muli pomwepo.
Lasanduka bwinja,
lagonjetsedwa ndi alendo.
8Mzinda wa Yerusalemu watsala wokhawokha
ngati nsanja m'munda wamphesa,
ngati dinda m'munda wa minkhaka,
ngatinso mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
9 Gen. 19.24; Aro. 9.29 Chauta Wamphamvuzonse
akadapanda kutipulumutsirako ena oŵerengeka,
tikadaonongeka kotheratu
ngati anthu a ku Sodomu ndi Gomora.
10Tsono imvani zimene Chauta akukuuzani,
inu akulu a ku Sodomu.
Mvetsetsani zimene Mulungu wathu akukuphunzitsani,
inu anthu a ku Gomora.
11 Amo. 5.21, 22 Chauta akuti,
“Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka?
Zandikola nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo
ndi za mafuta a nyama zonenepa.
Sindikuŵafunanso magazi a ng'ombe zamphongo
ndi a anaankhosa ndi a atonde.
12“Ndani amakulamulani
kuti mubwere nazo zimenezi pamaso panga?
Ndani amakuuzani
kuti muzipondaponda m'mabwalo a Nyumba yanga?
13Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe.
Utsi wake umandinyansa.
Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero,
kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata,
sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo.
14Zikondwerero zanu za pokhala mwezi
ndi masiku anu oyera ndimadana nazo.
Zasanduka katundu wondilemera,
ndatopa nako kuŵapirira.
15Mukamatambasula manja anu popemphera,
sindidzayang'anako.
Ngakhale muchulukitse mapemphero anu chotani,
sindidzasamalako,
chifukwa manja anu ndi odzaza ndi magazi.
16Sambani, dziyeretseni,
chotsani pamaso panga ntchito zanu zoipa.
Inde, lekani kuchita zoipa.
17Phunzirani kuchita zabwino.
Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize.
Tetezani ana amasiye,
muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
18Chauta akunena kuti,
“Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu:
chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri,
koma Ine ndidzakutsukani,
inu nkukhala oyera kuti mbee.
Mwachita kuti psuu ngati magazi,
koma mudzakhala oyera ngati thonje.
19Ngati muli okonzeka kundimvera,
mudzalidyera dziko.
20Koma mukakana ndi kumapanduka,
mudzaphedwa ndi lupanga.
Ine Chauta ndatero.”
Yerusalemu mzinda wodzaza ndi machimo21Taonanitu!
Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo,
tsopano ukuchita zadama.
Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro,
tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao.
22Iwe Yerusalemu, unali ngati siliva,
koma tsopano wasanduka wopandapake.
Unali ngati vinyo wabwino,
koma tsopano uli ngati vinyo
wosakanizika ndi madzi.
23Atsogoleri ako apanduka,
ndipo amagwirizana ndi mbala.
Aliyense amakonda chiphuphu,
ndipo amathamangira mphatso.
Satchinjiriza ana amasiye,
ndipo samvera madandaulo a akazi amasiye.
24Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,
Wamphamvu uja wa Israele, akunena kuti:
“Ha! Olimbana nane ndidzaŵatha,
adani anga ndidzaŵalipsira.
25Ndidzatambasula dzanja langa
kuti ndilimbane nawe.
Ndidzasungunula machimo ako nkuŵachotsa,
monga m'mene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
26Aweruzi ako ndidzaŵakhazikitsanso
ngati pa masiku akale aja.
Aphungu akonso ndidzaŵakhazikitsanso
ngati poyamba paja.
Pambuyo pake iweyo udzatchedwa mzinda waungwiro,
mzinda wokhulupirika.”
27Chauta ndi wolungama, adzaombola Ziyoni.
Chauta ndi waungwiro,
adzaombolanso anthu olapa amumzindamo.
28Koma opanduka ndi ochimwa adzaŵaonongera pamodzi,
osiya Chauta adzatheratu.
29Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu
imene inkakusangalatsani,
mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda
imene mudaipatula.
30Pakuti mudzafanafana
ndi mtengo wa thundu wofota masamba,
mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
31Anthu amphamvu adzasanduka ngati udzu wouma,
ntchito zao ngati mbaliŵali.
Motero anthuwo adzayakira limodzi ndi ntchito zaozo,
popanda woti auzimitse motowo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.