1Yuditi atatha kupemphera kwa Ambuye, atatsiriza mau onseŵa,
2adadzuka pamene adaagonapo, naitana mdzakazi wake, ndipo adatsikira m'nyumba mwake m'mene ankakhala pa masiku a Sabata ndi achikondwerero.
3Adavula chiguduli chake ndi zovala zake zaumasiye. Adasamba m'thupi, nadzola mafuta onunkhira amtengowapatali. Adapesa tsitsi lake, navala nduŵira yokongola kumutu. Adavalanso zovala zachimwemwe zimene ankavala, Manase mwamuna wake akali moyo.
4Adavala nsapato zake, mphete zake, ndolo zake zakukhutu ndi zinthu zake zonse zodzikongoletsera. Choncho adadzikongoletsa kwabasi, kuti azikopa anthu aamuna aliwonse okumana naye.
5Atatero, adasenzetsa mdzakazi wake botolo la vinyo, nsupa ya mafuta, thumba la ufa wabarele, keke lankhuyu ndi buledi wabwino. Zonsezo adazimanga mosamala, napatsira mdzakazi wake kuti anyamule.
6Atafika ku chipata cha mzinda wa Betuliya, adapeza Uziya ndi akuluakulu amumzinda aja, Kabrisi ndi Karmisi, akumdikira.
7Atampenya, nkuzindikira kuti nkhope yake yasintha, ndipo kuti zovala zake nzakaso, adadabwa ndi kukongola kwake.
8Adamuuza kuti, “Mulungu wa makolo athu akukomere mtima, akuthandize kuchita zimene watsimikiza mumtima mwako, kuti Israele apambane, ndipo Yerusalemu alemekezeke.”
9Yuditi adapembedza Mulungu chamumtima. Adauza akuluakuluwo kuti, “Lamulani anthuŵa kuti anditsekulire pa chipata, kuti ndituluke ndikachite zonse zimene takambirana zija.” Iwo aja adalamula anyamata kuti atsekule pa chipata monga m'mene adaapemphera.
10Yuditi adatuluka pa chipata, iye ndi mdzakazi wake. Anthu amumzindamo adamuyang'anitsitsa mpaka iye atatsika phiri ndi kufika m'chigwa, ndipo pambuyo pake sadamuwonenso.
11Akaziwo akuyenda m'chigwa, adakumana ndi kagulu ka asilikali a ku Asiriya.
12Iwowo adagwira Yuditi namufunsa kuti, “Kodi ndiwe wa mtundu wanji? Nanga ukuchokera kuti, ndipo ukupita kuti?” Iye adayankha kuti, “Ine ndine Muhebri, koma ndikuthaŵa anthu anga, chifukwa ndikudziŵa kuti mudzaŵagwira ndi kuŵapha.
13Ndikupita kwa Holofernesi, mtsogoleri wamkulu wankhondo, kuti ndikamuululire zoona zina ndi kumdziŵitsa njira ina yodzeramo, kuti akalande dziko lonse la mapirili, popanda ndi mmodzi yemwe mwa anthu ake kugwidwa kapena kuphedwa.”
14Anthuwo atamva mau amenewo, adayang'ana nkhope yake, ndipo adadodoma nako kukongola kwake.
15Adati, “Wapulumutsa moyo wako potsikira kwa mbuye wathu. Pita ku hema lake mwamsanga. Enafe tikuperekeza kuti tikakutule.
16Ukakafika pamaso pake, usakachite mantha, ukangomuuza zimene watifotokozerazi ndipo iyeyo akakuchitira zabwino.”
17Adasankha anthu 100 kuti amperekeze iye ndi mdzakazi wake, ndipo iwo adafika ndi akazi aŵiriwo ku hema la Holofernesi.
18Mbiri yakuti kwafika Yuditi itamveka ku hema lililonse, anthu ambiri adabwera kuchokera ku mbali zonse. Adamzungulira ataima pakhomo pa hema la Holofernesi. Ankangodikira pamene anthu aja ankauza Holofernesi za iyeyo.
19Kukongola kwake kodabwitsa kudaŵaganizitsa kuti Aisraele ndi anthu abwino kwambiri. Adayamba kufunsana kuti, “Ndani angathe kunyoza mtundu wa anthu umene uli ndi akazi okongola chotere? Tisasiyepo munthu ndi mmodzi yemwe. Tikangoŵalekerera, adzatha kukopa dziko lonse lapansi.”
20Choncho alonda a Holofernesi ndi anthu ake omtumikira, adatenga Yuditi naloŵa naye m'hema.
21Holofernesi ankapumula pa bedi, m'kati mwa nsalu zochingira, zoluka ndi thonje lofiirira ndi lagolide, zopetedwa ndi emeradi ndi timiyala tina tamtengowapatali.
22Anthu atamuuza za Yuditi, Holofernesi adatuluka nkudzaima pakhomo pa hema lake, patsogolo pake pali anthu onyamula nyale zasiliva.
23Yuditi atafika pamaso pa Holofernesi ndi atumiki ake, onsewo adadodoma nako kukongola kwake. Pamenepo Yuditi adagwadira ndi kulambira Holofernesi, koma atumiki a Holofernesi adamuimiritsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.