1Tsiku lina Afarisi ena pamodzi ndi aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaachokera ku Yerusalemu, adasonkhana kwa Yesu.
2Iwo adaaona kuti ophunzira ake ena ankangodya chakudya osasamba m'manja moyenera (ndiye kuti mosasamala mwambo wosamba m'manja.)
3Pajatu Afarisi ndi Ayuda ena onse saadya asanasambe m'manja mwa njira yoyenera. Amatero kuti asunge mwambo wa makolo.
4Ndipo akachokera ku msika, saadya osasamba m'manja. Amasunganso miyambo ina yambiri imene makolo ao adaŵasiyira, monga kutsuka zikho, miphika, ndi ziŵiya zamkuŵa
5Choncho Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo aja adamufunsa Yesu kuti, “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo, koma amangodya chakudya osasamba m'manja moyenera?”
6Yes. 29.13 Yesu adaŵayankha kuti, “Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaalemba kuti,
“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe,
koma mtima wao uli kutalitali ndi Ine.
7Amandipembedza inde,
koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu,
chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni,
ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
8Kenaka Yesu adati, “Inu mumasiya Malamulo a Mulungu, nkumasunga miyambo ya anthu.”
9Tsono popitiriza mau, Yesu adati, “Koma ndiye muli ndi njira yanu yochenjera yosiyira Malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu.
10Eks. 20.12; Deut. 5.16; Eks. 21.17; Lev. 20.9 Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
11Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni zasanduka Korobani,” (ndiye kuti zoperekedwa kwa Mulungu),
12ameneyo sasoŵanso kuŵathandiza atate ake ndi amai ake.’
13Pakutero mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe, chifukwa cha mwambo wanu umene mumasiyirana. Ndipo mumachita zinanso zambiri zotere.”
Za zinthu zimene zimaipitsa munthu(Mt. 15.10-20)14Pambuyo pake Yesu adaitananso anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani nonsenu, ndipo mumvetse bwino.
15Palibe chinthu chochokera kunja ndi kuloŵa m'kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.”
[
16“Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”]
17Pamene Yesu adasiya khamu lija la anthu nakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa za fanizo limeneli.
18Iye adaŵayankha kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? Kodi simukudziŵa kuti chilichonse chochokera kunja, ndi kuloŵa mwa munthu, sichingathe kumuipitsa?
19Pajatu sichiloŵa mumtima mwake, koma m'mimba, pambuyo pake nkumakatayidwa ku thengo.” (Pakunena zimenezi, Yesu adagamula kuti zakudya zonse anthu angathe kuzidya.)
20Adatinso, “Zimene zimatuluka mwa munthu, ndizo zimamuipitsa.
21Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana,
22zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa.
23Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”
Za chikhulupiriro cha mai wina(Mt. 15.21-28)24Yesu adanyamuka kupita ku dera la ku Tiro. Adakakhala kunyumba kwina, ndipo sadafune kuti anthu adziŵe kuti ali kumeneko. Komabe sadathe kubisika.
25Nthaŵi yomweyo mai wina, amene mwana wake wamkazi ankavutika ndi mzimu woipa, adamva za Iye. Adabwera kwa Yesu nagwada kumapazi kwake.
26Maiyo anali mkunja, wa mtundu wa anthu a ku Siro-Fenisiya. Adapempha Yesu kuti akatulutse mzimu woipawo mwa mwana wake.
27Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ai, alekeni ana ayambe adya nkukhuta. Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.”
28Apo maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amakhala m'munsi mwa tebulo nkumadyako nyenyeswa zimene ataya ana?”
29Apo Yesu adamuuza kuti, “Chifukwa cha mau mwanenaŵa, pitani, mzimu woipawo watuluka mwa mwana wanu.”
30Mai uja adabwerera kunyumba kwake, nakapezadi mwanayo ali gone pa bedi, mzimu woipa uja utatuluka.
Yesu achiritsa gonthi31Yesu adachokanso ku dera lija la ku Tiro, namayenda kudutsa dera la ku Sidoni, kupita ku nyanja ya ku Galileya, kudzera pakati pa dera la Mizinda Khumi.
32Anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu yemwe anali gonthi ndi wolankhula movutikira. Anthuwo adapempha Yesu kuti amchiritse pomusanjika manja munthuyo.
33Yesu adatengera munthu uja pambali kumchotsa pa khamu la anthu. Adapisa zala m'makutu a munthuyo, nalavula malovu, nkukhudza lilime la munthu uja.
34Adayang'ana kumwamba, nadzuma, nkumuuza kuti, “Efata!” ndiye kuti “Tsekuka!”
35Pomwepo makutu a munthuyo adatsekuka, ndipo chimene chinkamanga lilime lake chidamasuka, mpaka adayamba kulankhula bwino lomwe.
36Yesu adalamula anzake a munthuyo kuti, “Musakauzetu wina aliyense zimenezi.” Koma ngakhale adaŵaletsa mwamphamvu choncho, iwo adanka nalengeza ndithu zimenezi.
37Ndipo anthu adazizwa kopitirira ndithu. Adati, “Ameneyu amachita zonse bwino. Ngakhale agonthi amaŵachiritsa nkumamva, ndipo osalankhula amaŵalankhulitsa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.