1Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa kufuna kwa Mulungu. Adandituma kuti ndilalike chilonjezo cha moyo umene uli mwa Khristu Yesu.
2 Ntc. 16.1 Ndikulembera iwe Timoteo, mwana wanga wokondedwa. Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu akukomere mtima, akuchitire chifundo ndi kukupatsa mtendere.
Paulo athokoza Mulungu3Ndikuthokoza Mulungu amene ndimamtumikira ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, monga momwe ankachitira makolo anga. Ndimamthokoza ndikamakukumbukira kosalekeza m'mapemphero anga usana ndi usiku.
4Ndikamakumbukira misozi yako, ndimafunitsitsa kukuwona, kuti ndikhale ndi chimwemwe chodzaza.
5Ntc. 16.1Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho.
Paulo alimbitsa Timoteo mtima6Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto.
7Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
8Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m'ndende chifukwa cha iye, koma umve nao zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu za Mulungu.
9Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe.
10Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m'kuwoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. Khristuyo adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse.
11 1Tim. 2.7 Mulungu adandiika kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwino umenewu,
12nchifukwa chake ndilikumva masautsoŵa. Koma sindichita manyazi, pakuti ndimamdziŵa Iye amene ndakhala ndikumkhulupirira, ndipo sindikayika kuti Iyeyo angathe kusunga bwino, mpaka tsiku la chiweruzo, zimene adandisungiza ine.
13Uŵagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti uzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu.
14Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.
15Ukudziŵa kuti onse a ku dziko la Asiya adandisiya. Mwa iwowo wina ndi Figelo, wina ndi Heremogene.
16Ambuye achitire chifundo banja la Onesifore, chifukwa iye ankandisangulutsa kaŵirikaŵiri. Sankachita nane manyazi, ngakhale ndinali womangidwa ndi unyolo:
17adangoti atafika ku Roma, nkuyamba kundifunafuna mwachangu, mpaka adandipeza.
18Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Mulungu pa tsiku la chiweruzo. Ukudziŵa bwino ndi iwe wemwe kuti adandithandiza kwambiri ku Efeso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.