1 Am. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chaka cha 151 Demetriyo, mwana wa Seleuko, adanyamuka ku Roma, nkuwoloka nyanja pamodzi ndi anthu oŵerengeka nakafika pa mzinda wina wapanyanjapo. Pamenepo adayamba kulamulira.

2Pamene ankaloŵa m'nyumba yachifumu ya makolo ake, gulu lankhondo lidagwira Antioko ndi Lisiyasi kubwera nawo kwa iye.

3Atamva zimenezo iyeyo adati, “Ndisaŵaone m'maso anthu amenewo.”

4Choncho ankhondo aja adaŵapha, Demetriyo nkukhala pa mpando waufumu.

5Tsono kudafika anthu oipa ndi okana chipembedzo a ku Israele. Mtsogoleri wao anali Alikimo, amene ankafuna kukhala mkulu wa ansembe.

6Anthuwo adayamba kusinjirira mtundu wao pamaso pa mfumu, nkumanena kuti, “Yudasi ndi abale ake adapha abwenzi anu onse, ndipo ifeyo adatipirikitsa m'dziko lathu.

7Ndiye inu mutumize munthu amene mumamkhulupirira, kuti akaone zoipa zimene Yudasi adatichita, ndi zimene adalichita dziko la mfumu. Tsono akaŵalange iwowo ndi ena onse oŵathandiza.”

8Mwa abwenzi ake mfumu idasankhula Bakide, bwanamkubwa wa dziko la patsidya pa mtsinje, munthu wotchuka m'dziko ndi wokhulupirika.

9Adamtuma pamodzi ndi Alikimo waupandu uja, amene adaamsandutsa mkulu wa ansembe onse, namlamula kuti aŵathire msimsi Aisraele.

10Iwowo adanyamuka ndi gulu lalikulu lankhondo nakaloŵa m'dziko la Yudeya. Adatuma amithenga kwa Yudasi ndi abale ake kukaŵauza mau onama onena za mtendere.

11Koma iwowo, ataona kuti afika ndi gulu lalikulu lankhondo, sadaŵakhulupirire mau aowo.

12Komabe alembi ena adadza kwa Alikimo ndi kwa Bakide kudzapempha chipangano chachilungamo.

13Pakati pa Aisraele, Asidea ndiwo adaayamba kupempha za mtendere.

14Ankati, “Pabwera wansembe wina wa fuko la Aroni, wadza ndi gulu lankhondo. Koma iyeyo sadzatichita zoipa.”

15Wansembeyo adakamba nawodi mau amtendere, naŵalonjeza molumbira kuti, “Sitifuna kukuchitani zoipa, inu ndi abwenzi anu.”

16Iwowo adamumvera, koma iye adagwira anthu makumi asanu ndi limodzi mwa iwo, nalamula kuti aphedwe pa tsiku limodzi. Choncho mau a Mulungu adapherezera, onena kuti,

17 .

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help