Mas. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuthokoza Mulungu chifukwa cha chilungamo chakeKwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo yoti:Imfa ya Mwana. Salmo la Davide.

1Ndidzakuthokozani, Inu Chauta,

ndi mtima wanga wonse.

Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.

2Ndidzakondwa ndi kusangalala

chifukwa cha Inu,

ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu,

Inu Wopambanazonse.

3Mukangofika, adani anga amathaŵa,

amaphunthwa ndi kufa pamaso panu.

4Inu mwatsimikiza kusalakwa kwanga.

Mwakhala pa mpando woweruza,

mwagamula kuti ndine wosapalamula.

5Mwaimba mlandu mafuko a anthu,

mwaononga anthu oipa.

Adzaiŵalika mpaka muyaya.

6Adani athu atha phu.

Mwapasula mizinda yao kotheratu,

anthu sadzaikumbukiranso.

7Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu

nthaŵi zonse,

adakhazika mpando wake kuti aziweruza.

8Iye amaweruza dziko lapansi molungama,

amagamula milandu ya anthu mosakondera.

9Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa,

ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.

10Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta,

amakukhulupirirani,

pakuti Inu Chauta simuŵasiya

anthu okufunitsitsani.

11Imbani nyimbo zotamanda Chauta

amene amakhala ku Ziyoni.

Lalikani za ntchito zake

kwa anthu a mitundu yonse.

12Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika,

salephera kumva kulira kwao

ndipo amalanga anthu oŵazunzawo.

13 Lun. 16.13 Mundikomere mtima, Inu Chauta.

Onani m'mene akundisautsira anthu ondida.

Inu mumandipulumutsa ku imfa,

14kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse,

pakati pa anthu anu a mu Ziyoni.

Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa.

15Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe.

Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika

wotcha iwo omwe.

16Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama,

koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.

17Tsono anthu oipa adzapita

ku dziko la anthu akufa,

ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.

18Koma anthu aumphaŵi

Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse,

anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala

mpang'ono pomwe.

19Dzambatukani, Inu Chauta,

munthu asakunyozeni.

Azengeni mlandu anthu akunja.

20Inu Chauta, aopseni anthuwo.

Akunjawo adziŵe kuti iwo ndi anthu chabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help