Tob. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tobiyasi afika kwa Raguele

1Ataloŵa ku Ekibatana, Tobiyasi adati, “Azariyasi, mbale wanga, undiperekeze msanga ku nyumba ya Raguele mbale wathu.” Adapita nayedi ku nyumba ya Raguele. Adampeza atakhala pansi pafupi ndi khomo loloŵera ku bwalo lake, nayamba ndiwo kumpatsa moni. Iye adaŵauza kuti, “Abale anga, ndakulandirani ndi manja aŵiri kwathu kuno.” Atatero adaŵaloŵetsa m'nyumba mwake.

2Raguele adauza Edina, mkazi wake, kuti, “Taona, mnyamatayu akufanafana ndi Tobiti mbale wathu.”

3Edina adaŵafunsa kuti, “Kodi mwachokera kuti, abale?” Iwo adayankha kuti, “Ndife ana a Nafutali, tidatengedwa ukapolo kupita ku Ninive.”

4Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi Tobiti, mbale wathu mumamdziŵa?” Iwo adayankha kuti, “Inde timaŵadziŵa.”

5Edina adafunsanso kuti, “Nanga ali bwanji?” Iwo adayankha kuti, “Ali moyo ndipo ali bwino.” Tobiyasi adati, “Amene aja ndi abambo anga.”

6Gen. 33.4; 45.14; Lk. 15.20Tsono Raguele adadza pafupi nampsompsona, misozi ili m'maso.

7Ndipo adati, “Mulungu akudalitse, iwe mwana wanga, mwana wa bambo waulemu. Koma nzomvetsa chisoni kuti iyeyo amene ali munthu wolungama ndi wa ntchito zabwino, adachita khungu.” Adakumbatira Tobiyasi mbale wake, nalira misozi.

8Edina mkazi wake ndi Sara mwana wake nawonso adayamba kulira chifukwa cha Tobiti. Raguele adapha nkhosa, pofuna kulandira alendowo mwaufulu.

Iwo adasamba nakakhala podyera. Tsono Tobiyasi adauza Rafaele kuti, “Azariyasi, mbale wanga, muuzetu Raguele zijazi zoti andipatse Sara mlongo wangayu, ndimkwatire.”

9Raguele adamva mauwo, nauza mnyamatayo kuti,

10“Yamba wadya ndi kumwa, usangalale madzulo ano. Palibe wina woti nkukwatira mwana wanga, Sara. Palibe winanso, koma iweyo mbale wanga basi. Ndipo ine sindingathe kumkwatitsa kwa wina, popeza kuti iwe wekha ndiye msuweni wake weniweni. Komatu mwana wanga, iwe wekha ndisakubisire kanthu.

11Ndidamukwatitsapo kale kwa amuna asanu ndi aŵiri, ndipo onsewo adafa usiku womwe adaloŵana nayewo. Koma tsopano, mwana wanga, idya ndi kumwa, ndithu Ambuye akusungani.”

12Tobiyasi adayankha kuti, “Koma ine sindidya ndi kumwa kanthu mpaka mutatsiriza nkhani yangayi.” Raguele adati, “Chabwino, zitero. Ndimpereka kwa iwe, monga momwe zidalembedwera m'buku la Mose. Mulungu wakumwamba adafuna kuti ndimpereke kwa iwe. Mlandire tsono mlongo wakoyo. Kuyambira tsopano ndiwe mchimwene wake, iyeyo ndi mlongo wako. Ndikumpereka kwa iwe lero kuti akhale wako nthaŵi zonse. Ndipo Ambuye akumwamba akudalitseni usiku uno, mwana wanga, akupatseni chimwemwe ndi mtendere.”

Mwambo waukwati

13Raguele adaitana Sara mwana wake. Iyeyo atabwera, adamgwira dzanja nampereka kwa Tobiyasi. Adauza Tobiyasiyo kuti, “Mlandire monga kudalembedwera m'buku la Mose kuti akhale mkazi wako. Umtenge upite naye ali wamoyo kwa bambo wako. Ndipo Mulungu wakumwamba akupatseni chimwemwe ndi mtendere!”

14Tsono adapempha amai a Sarayo kuti abwere ndi cholemberapo. Choncho adalembapo za chipangano cha ukwati, chakuti wapereka mwana wake Sara kuti akhale mkazi wa Tobiyasi, potsata zimene zidalembedwa m'buku la Mose.

15Kenaka adayamba kudya ndi kumwa.

16Tsono Raguele adaitana Edina, mkazi wake, namuuza kuti, “Ukonze chipinda china, kuti Sara aloŵemo.”

17Adapita kukakonza bedi m'chipindamo monga momwe adaamuuzira, namuloŵetsamo. Adamlirira misozi; pambuyo pake atapukuta misozi yakeyo, adati,

18“Ukhulupirire, mwana wanga! Ambuye akumwamba akupatse chimwemwe m'malo mwa chisoni! Ukhulupirire, mwana wanga!” Ndipo Edina adatuluka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help