Mla. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zochita za munthu wanzeru

1Ndalama zako uziike pa malonda

okagulitsa kutsidya kwa nyanja,

ndipo udzapeza phindu patapita masiku ambiri.

2Ndalama zako uzisungize pa malo angapo,

malo ambiri ndithu,

pakuti sukudziŵa choipa

chimene chidzaoneke pa dziko lapansi.

3Mitambo ikadzaza ndi madzi, kumagwa mvula.

Mtengo ukagwera chakumwera kapena chakumpoto,

kumene wagwerako kogonera nkomweko.

4Amene ayembekeza kuti mphepo ikhale bwino,

kapena kuti mitambo ibwere bwino,

sadzabzala ndipo sadzakolola kanthu.

5M'mene mzimu umaloŵera m'thupi la mwana m'mimba mwa mkazi wodwala, inu simudziŵa. Chonchonso ntchito ya Mulungu amene amapanga zonse, inu simungaidziŵe.

6M'maŵa uzifesa mbeu zako, ndipo madzulo usamangoti manja lende. Sudziŵa chimene chidzapindula, kaya ndi ichi kaya ndi chinachi, mwinanso ziŵiri zonsezo zitha kukhala zabwino.

7Kuŵala kwam'maŵa kumasangalatsa, ndipo maso ako akaona dzuŵa amakondwa.

8Munthu akakhala wa zaka zambiri, mlekeni akondwerere zaka zonsezo. Koma azikumbukira kuti masiku otsatira imfa yake ndi ochuluka koposa. Zonse zikudzazi nzopanda phindu.

Malangizo kwa achinyamata

9Anyamata inu, muzikondwerera unyamata wanu. Mitima yanu izisangalala pa nthaŵi ya unyamata wanu. Inde muzitsata zimene mtima wanu ukufuna, ndiponso zimene maso anu akupenya. Koma mudziŵe kuti pa zonsezo Mulungu adzakuweruzani.

10Choncho muchotseretu zokusautsani mu mtima mwanu, mupewe zokupwetekani m'thupi mwanu. Pajatu unyamata ndi ubwana, zonse nzopandapake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help