1Saulo atabwerako kumene ankamenyana ndi Afilisti kuja, adamva kuti Davide ali ku chipululu cha Engedi.
2Tsono adatenga ankhondo okhoza zedi 3,000 amene adaŵasankha pakati pa ankhondo onse. Adapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale.
3Mas. 57; 142Adafika ku makola a nkhosa a pamphepete pa njira, pamene panali phanga. Saulo adaloŵa m'phangamo kuti akadzithandize. Pamenepo nkuti Davide ndi anthu ake akubisala m'kati mwenimweni mwa phangalo.
4Apo anthu a Davide aja adamuuza kuti, “Tsiku lija ndi lero limene Chauta ankanena, muja adaakuuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wako m'manja mwako, udzamchita zomwe zidzakukomere.’ ” Tsono Davide adanyamuka, nakadulako chidutswa ku mkanjo wa Saulo, iyeyo osadziŵako ai.
5Koma pambuyo pake Davideyo adavutika mumtima mwake, chifukwa chakuti anali atadula chidutswa chija ku mkanjo wa Saulo.
61Sam. 26.11 Tsono adauza anthu ake kuti, “Chauta andiletse kumchita choipa mbuyanga, wodzodzedwa wa Chauta. Ndisampweteke, popeza kuti ngwodzozedwa wa Chauta.”
7Choncho Davide atalankhula mau ameneŵa, anthu ake adamvera, pakuti sadaŵalole kuti amthire nkhondo Saulo. Pamenepo Saulo adatuluka m'phanga muja namapita.
8Pambuyo pake Davide nayenso adatuluka m'phangamo, ndipo adaitana Saulo kuti, “Mbuyanga mfumu.” Saulo atacheuka, Davide adamgwadira pogunditsa nkhope yake pansi.
9Adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani mumamvera mau a anthu amene amanena kuti, ‘Davide akufuna kukuphani?’
10Lero mwaonatu ndi maso anu kuti Chauta anakuperekani m'manja mwanga m'phanga muja. Ena ankandikakamiza kuti ndikupheni, koma ndakulekani dala. Ndinati, ‘Sindipweteka mbuyanga, poti ngwodzozedwa wa Chauta.’
11Atate anga, onanitu chidutswa cha mkanjo wanu chili m'manja mwangachi. Pamenepo mudziŵe kuti mumtima mwanga mulibe cholakwa kapena zokuukirani, poti ndadula chidutswa ku mkanjo wanu, koma osakuphani. Sindidakulakwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.
12Chauta aonetse kuti wolakwa ndani pakati pa ine ndi inu. Akulangeni chifukwa cha zimene mukundichitazi. Koma ine sindikupwetekani, ai.
13Paja anthu akale adati, ‘Munthu woipa, ntchito zake nzoipa.’ Motero ine sindikupwetekani, ai.
141Sam. 26.20 Kodi mfumu ya Israele yadzalondola yani? Kodi ikufuna kugwira yani? Zedi, mukulondola ine galu wakufa! Mufuna kupha ine nthata!
15Nchifukwa chake Chauta aweruze, ndipo agamule pakati pa ine ndi inu kupeza wolakwa. Anditeteze. Aonetse kulungama kwanga pondipulumutsa kwa inu.”
16Davide atamaliza kulankhula mau ameneŵa, Saulo adafunsa kuti, “Kani liwu limeneli ndi lakodi, mwana wanga Davide?” Apo Saulo adayamba kulira mokweza.
17Adauza Davide kuti, “Iwe wachita chilungamo kupambana ine, pakuti wandichitira ine zabwino pamene ine ndakuchita zoipa.
18Lero waonetsa ubwino wako pakuti sudandiphe, Chauta atandipereka kwa iwe.
19Kodi munthu atapeza mdani wake, angalole kuti mdaniyo apulumuke? Motero Chauta akuchitire zabwino, chifukwa cha zimene wandichitira lerozi.
20Ona tsono, ndikudziŵa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndipo kuti ufumu wa Israele udzakhazikika pa iwe.
21Undilonjeze molumbira tsono m'dzina la Chauta kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira, kuti dzina langa ndi la abambo anga lisaiŵalike.”
22Davide adalumbira zonsezi Saulo alikumva. Tsono Saulo adabwerera kwao, koma Davide ndi anthu ake adapitanso kuphanga kobisalira kuja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.