Esr. A - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Maloto a Mordekai 1 Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Ahasuwero, mfumu yaikulu, tsiku loyamba mwezi wa Nisani, Mordekai, mwana wa Yairo, mwana wa Semei, mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini, adaalota maloto. 2 Mordekai anali Myuda wokhala mu mzinda wa Susa. Anali munthu wotchuka ndipo ankatumikira m'nyumba ya mfumu. 3 Anali mmodzi mwa anthu amene Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaaŵatenga ukapolo kuŵachotsa ku Yerusalemu, pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya ku Yudeya. 4 Maloto ake anali otere: Kudaamveka phokoso lalikulu, mabingu, chivomezi ndi chisokonezo pa dziko lapansi. 5 Pomwepo padafika dzinjoka dzikuludzikulu dziŵiri dzikukonzekera kuyambana, ndipo dzinkachita phokoso loopsa. 6 Pakumva phokosolo, mitundu yonse ya anthu idakonzekera nkhondo, nkhondo yake yolimbana ndi fuko la anthu olungama. 7 Linalitu tsiku lamdima ndi lamavuto, latsoka ndi lodetsa nkhaŵa, lamazunzo ndi la chisokonezo chachikulu pa dziko lapansi. 8 Anthu olungama onse aja adaavutika mu mtima chifukwa choopa zoipa zimene zinkati zidzaŵagwere. Mwakuti anali okonzeka kuti afe. 9 Koma adalira kwa Mulungu kuti aŵathandize. Tsono chifukwa cha kulira kwaoko, adangoona kuti ngati pa kasupe wamng'ono pakutuluka mtsinje waukulu wodzaza ndi madzi. 10 Kutacha, ndipo dzuŵa litatuluka, anthu ofooka aja adalandira mphamvu, ndipo adaononga adani ao odzikuza aja. 11 Atalota maloto ameneŵa, ndipo atazindikira zimene Mulungu adaakonzeratu kuti achite, Mordekai adadzuka. Tsono adasunga malotowo mumtima mwake nayesayesa tsiku lonselo kumvetsetsa tanthauzo lake.Mordekai apulumutsa moyo wa mfumu 12 Mordekai adaazoloŵera kupumula m'bwalo la mfumu, pamodzi ndi Bigitana ndi Teresi, afule aŵiri a mfumu amene ankalonda m'bwalomo. 13 Tsiku lina adaŵamva akukambirana. Iye pofufuza nkhaniyo, adazindikira kuti anthu aŵiriwo anali ndi cholinga cha kuukira mfumu Ahasuwero. 14 Tsono Mordekai adadziŵitsa mfumu za cholinga chaocho. Mfumu itaŵafunsitsa, iwo adaulula chifuniro chao choipacho; choncho mfumu idalamula kuti aphedwe. 15 Kenaka mfumu idalembetsa zimenezi m'buku la Mbiri. Mordekai nayenso adazilemba. 16 Pambuyo pake mfumu idalamula kuti Mordekai akhale ndi udindo m'bwalo la mfumu, ndipo kuti alandire mphotho pa zimene adaachitazo. 17 Koma Mwagagi wina dzina lake Hamani, mwana wa Hamedata, amene mfumu inkamlemekeza kwakukulu, ankafunitsitsa kuchita chiwembu Mordekai ndi fuko lake, chifukwa cha zimene Mordekaiyo adaaŵachita afule aŵiri aja.