Miy. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Wosauka amene amayenda molungama

amaposa munthu wopusa wolankhula zokhota.

2Si bwino kuti munthu akhale wosadziŵa zinthu,

ndipo munthu woyenda mofulumira dziŵi amasokera.

3Kupusa kwake kwa munthu kukamgwetsa m'chiwonongeko,

mtima wake umadzakwiyira Chauta.

4Chuma chimachulukitsa abwenzi atsopano,

koma wosauka abwenzi ake amamthaŵa.

5Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,

wolankhula mabodza sadzapulumuka.

6Ambiri amafuna kuti munthu wopata aŵakomere mtima,

munthu wooloŵa manja amakhala bwenzi la anthu onse.

7Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye,

nanji abwenzi ake tsono!

Iwo ndiye adzamthaŵira kunka kutali.

Amayesetsa kuŵalondola mopembedzera, koma osaŵathanso.

8Amene amakonda nzeru amadzichitira zabwino mwiniwakeyo.

Amene ali womvetsa, zinthu zidzamuyendera bwino.

9Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,

wolankhula mabodza adzaonongeka.

10Nkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wachuma,

nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!

11Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga,

ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

12Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango,

koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.

13Mwana wopusa ndi tsoka kwa atate ake,

mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi.

14Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo,

koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.

15Ulesi umagonetsa tulo tofa nato,

choncho munthu waulesi adzavutika ndi njala.

16Munthu womvera malamulo amadzisungira moyo,

koma munthu wonyoza malangizo a Mulungu adzafa.

17Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza

Chauta,

ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera

chifukwa cha ntchito zake.

18Uzimlanga mwana wako chikhulupiriro chikadalipo,

ukapanda kutero, wamuwononga.

19Munthu wa ukali woopsa adzalandira

chilango chomuyenerera,

pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale.

20Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo,

kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

21Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri,

koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.

22Chofunika kwa munthu nkukhulupirika.

Kukhala wosauka nkwabwino koposa kukhala wonama.

23Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo,

ndipo amene amaopayo amakhala pabwino,

ndiye kuti choipa sichidzamgwera.

24Waulesi amati akapisa dzanja m'mbale,

kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake.

25Ukamenya munthu wonyoza anzake, adzachenjererapo.

Ukadzudzula munthu womvetsa bwino zinthu,

adzapindulapo nzeru.

26Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa

amai ake,

ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi

ndiponso wonyozetsa.

27Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,

udzapatukana ndi mau opatsa nzeru.

28Mboni yachabe imanyoza chilungamo,

pakamwa pa anthu oipa pamalikwira tchimo.

29Zakonzeka kale kuti mlandu uŵagwere anthu onyoza,

mkwapulo ndi wokonzakonza kuti akwapulire

pamsana pa zitsiru.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help