1 Yes. 13.1—14.23; 47.1-15 Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya kunena za mzinda wa Babiloni ndi anthu ake. Adati,
2“Ulengeze ndi kulalika kwa anthu a mitundu yonse.
Kweza mbendera ndipo usabise kanthu, uŵauze kuti,
‘Babiloni wagwa!
Mulungu wake Beli wachititsidwa manyazi,
nayenso Merodaki wataya mtima.
Mafano ake anyozedwa kwambiri,
milungu yake yataya mtima.’
3“Mtundu wa anthu akumpoto wadzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Dziko lake adzalisandutsa bwinja, ndipo kumeneko sikudzakhalanso munthu kapena nyama.”
Za kubwerera kwa Israele4Chauta akunena kuti, “Masiku amenewo, nthaŵi imeneyo Aisraele ndi Ayuda adzasonkhana pamodzi, azikabwera nalira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Chauta Mulungu wao afuna.
5Adzafunsa njira ya ku Ziyoni, nkuyamba ulendo wobwerera kumeneko. Adzati, ‘Tiyeni tibwerere kwa Chauta, tikachite naye chipangano chamuyaya, chimene sichidzaiŵalika konse.’
6“Anthu anga anali ngati nkhosa zotayika. Abusa ao adaŵasokeza ndi kuŵayalukitsa ku mapiri. Ankangoyendayenda ku zitunda ndi ku mapiri, mpaka kuiŵala kwao.
7Aliyense amene adaŵapeza, adaŵaononga. Ndipo adani ao ankati, ‘Ifetu tilibe mlandu, chifukwa choti iwoŵa adachimwira Chauta amene ndiye pokhala pao penipeni, amenenso makolo ao ankamkhulupirira.’
8 Chiv. 18.4 “Thaŵaniko ku Babiloni. Chokaniko ku dziko la Ababiloni, muyambe ndinu kutuluka, ngati atonde otsogolera ziŵeto.
9Ndidzasankha ndi kubwera nalo gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ya anthu lochokera kumpoto, kuti lidzamenyane ndi Babiloni. Mivi yao ili ngati ya wankhondo waluso, yosapita padera.
10Ababiloni adzafunkhidwa, ndipo onse oŵafunkha adzakhuta,” akutero Chauta.
Za kugwa kwa Babiloni11“Inu Ababiloni, mudaononga anthu anga osankhidwa.
Ngakhale mukondwe ndi kusangalala,
ngakhale mulumphelumphe mokondwa ngati
mwanawang'ombe wopuntha tirigu,
ngakhale mulire monyada ngati akavalo,
12mzinda wanu udzachititsidwa manyazi ndithu kwambiri.
Mzinda umene uli ngati mai wanu adzaunyazitsa.
Ndithudi, Ababiloni adzakhala otsirizira mwa
anthu a mitundu yonse.
Mzinda wao udzakhala ngati thengo,
ngati dziko louma lachipululu.
13Udzakhala wopanda anthu chifukwa cha mkwiyo wa Chauta,
udzakhala chipululu chokhachokha.
Onse odutsa ku Babiloni azidzachita nyansi,
nkumangotsonya chifukwa cha mabala a mzindawo.
14Konzekani kuti mumzinge Babiloni pa mbali zonse,
inu okoka mauta.
Mlaseni, chulukitsani mivi yanu.
Iye uja adachimwira Chauta.
15Mfuulireni ponseponse pakuti wagonja.
Nsanja zake zagwa, malinga ake aonongeka.
Kumeneku ndiko kulipsira kwa Chauta.
Mlipsireni, mumchite zonga zomwe iye adaŵachita ena.
16Ku Babiloniko chotsani wofesa aliyense
ndiponso aliyense wodula tirigu ndi
chikwakwa chake pa nthaŵi yokolola.
Poopa lupanga la ozunza anzao,
aliyense adzatembenukira kwa anthu ake,
nkuthaŵira ku dziko lakwao.”
Za kubwerera kwa Israele17Aisraele ali ngati nkhosa zomwazika, zopirikitsidwa ndi mikango. Mfumu ya ku Asiriya ndiyo idayamba kuŵapha Aisraelewo, nkudzabwera Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni kudzachita ngati kupwepweta mafupa ao.
18Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi dziko lake, monga momwe ndidalangira mfumu ya ku Asiriya.
19Israele ndidzambwezera kubusa kwake, ndipo azikadya ku Karimele ndi ku Basani. Adzadya chakudya chokwanira ku mapiri a ku Efuremu ndi ku Giliyadi.
20Pa masiku amenewo, nthaŵi imeneyi ikadzafika, adzafunafuna zolakwa za Israele, koma sichidzapezeka nchimodzi chomwe. Adzafufuzafufuza machimo a Yuda, koma silidzapezeka nlimodzi lomwe. Pakuti otsala amene ndaŵasiya aja ndidzaŵakhululukira,” akutero Chauta.
Za Chilango cha Babiloni21“Lithireni nkhondo dziko la Merataimu
ndi anthu okhala ku Pekodi.
Muŵaphe ndi lupanga ndi kuŵaonongeratu.
Muchite zonse zimene ndakulamulani,”
akutero Chauta.
22“Phokoso la nkhondo likumveka m'dziko,
ndiponso pali chiwonongeko chachikulu.
23Amene anali ngati nyundo ya dziko lapansi uja,
onani m'mene aphwanyikira.
Onani m'mene Babiloni wasandukira chinthu
chonyansa pakati pa mitundu ya anthu.
24Iwe Babiloni, ndakutchera msampha ndipo wakodwamo,
iwe osazindikira kanthu.
Udapezeka ndipo udagwidwa
chifukwa chakuti udaalimbana ndi Chauta.
25Chauta watsekula nyumba ya zida zake,
ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake.
Paja Chauta Wamphamvuzonse ali ndi ntchito
yoti agwire ku dziko la Ababiloni.
26Mumenyane naye Babiloni mbali zonsezonse.
Tsekulani nkhokwe zake.
Anthu ake muŵaunjike ngati milu ya tirigu,
ndipo muŵaononge kotheratu,
pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
27Iphani anyamata ake onse ankhondo.
Onse aphedwe ndithu.
Tsoka laŵagwera pakuti tsiku lao la chilango lafika.”
28“Ndikumva anthu othaŵa nkhondo ya ku Babiloni akulengeza za kulipsira kwa Chauta, Mulungu wathu, kulipsirira chifukwa choononga Nyumba yake.”
29 Chiv. 18.6 “Muitane onse oponya mivi kuti amthire nkhondo Babiloni, abwerenso onse okoka mauta. Mzingeni ndi zithando zankhondo kuti asathaŵepo munthu ndi mmodzi yemwe. Mlangeni potsata zolakwa zake. Mchiteni zomwe iye adaŵachita ena. Iyeyu adanyoza Chauta, Woyera uja wa Israele.
30Nchifukwa chake anyamata ake adzagwa m'mabwalo ake. Ndipo ankhondo ake onse adzaonongeka tsiku limenelo,” akutero Chauta.
31“Ndikukuthira nkhondo, mzinda wachipongwewe,
pakuti yakwana nthaŵi yako,
lafika tsiku lako la chilango,”
akutero Chauta Wamphamvuzonse.
32“Mtundu wodzikuzawe, udzaphunthwa nkugwa,
ndipo palibe amene adzakudzutse.
Mizinda yako ndidzaitentha ndi moto,
motowo udzapsereza zonse zoyandikana nayo mizindayo.”
33Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu a ku Israele akuzunzidwa pamodzi ndi anthu a ku Yuda. Onse amene adaŵagwira ukapolo aŵagwiritsa, osafuna kuŵamasula.
34Koma mpulumutsi wao ndi wamphamvu, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Adzaŵaimira pa mlandu, kuti apatse mtendere dziko lonse lapansi, koma adzavutitsa okhala ku Babiloni.
35“Lupanga lankhondo lilunjika pa Ababiloni,
Imfa iloze pa anthu a ku Babiloni,
pa akuluakulu ao ndi pa anthu ao anzeru,”
akutero Chauta.
36“Lupanga lilunjike pa anthu oombeza,
kuti asanduke zitsilu.
Lilunjikenso pa ankhondo ake,
kuti aonongedwe.
37Lupanga lilunjike pa akavalo ake ndi pa magaleta ake,
lilunjikenso pa magulu ankhondo achilendo
amene ali pakati pao,
kuti asanduke ngati akazi.
Lupanga lilunjike pa chuma chake chonse,
kuti chidzafunkhidwe.
38Chilala chilunjike pa madzi ake,
kuti adzaphwe.
Paja dzikolo nlamafano,
anthu ake achita kuyaluka nawo mafanowo.
39 Chiv. 18.2 “Nchifukwa chake ku Babiloni nyama zakuthengo zizidzakhalira limodzi ndi afisi, ndipo nthiŵatiŵa zizidzakhalamonso. Tsono kumeneko sikudzakhala anthu mpaka muyaya. Sikudzapezeka munthu ndi mmodzi yemwe pa mibadwo yonse.
40Gen. 19.24, 25 Monga momwe Mulungu adaonongera Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yonse yozungulira, momwemonso palibe munthu amene adzakhale kumeneko. Palibe ndi mmodzi yemwe amene azidzayendako.
41“Onani, ankhondo akubwera kuchokera kumpoto.
Anthu a mtundu wanyonga ndi mafumu ambiri
akunyamuka kuchokera ku madera akutali
a dziko lonse lapansi.
42Atenga mauta ndi mikondo,
ngankhalwetu, ndiponso opanda chifundo.
Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja.
Akwera pa akavalo, atavala zankhondo,
kuti adzamenyane nawe, iwe mzinda wa Babiloni.
43Mfumu ya ku Babiloni idamva za mbiri yao,
ndipo yachita kuti m'nkhongono zii!
Yada nkhaŵa,
ikumva kuŵaŵa ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.
44“Monga momwe mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yordani umaopsera khola lankhosa lotetezedwa bwino, Inenso mwadzidzidzi ndidzapirikitsira Ababiloni kutali ndi kwao. Pambuyo pake ndidzaŵaikira woŵalamulira amene ndidzamufune Ine. Nanga ndani angafanefane ndi Ine? Ndani angandipititse ku bwalo lamilandu? Ndi mtsogoleri uti amene angalimbike pamaso panga?
45Nchifukwa chake imvani, zimene Ine Chauta ndakonza zolangira Babiloni, ndiponso zolinga zanga zolangira dziko la Ababiloni ndi izi: Ndithudi, ndi ana omwe adzatengedwa, ndipo onse adzada nalo nkhaŵa tsoka lao.
46Dziko lonse lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha kugwa kwa Babiloni. Kulira kwake kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.