1Ha! Golide wathu tsopano wathimbirira kwambiri.
Golide wathu wosalala uja wasinthika kotheratu.
Miyala ya ku malo oyera yamwazikana,
ili vuu, ku mphambano zonse za miseu.
2Onani ana okondedwa a m'Ziyoni
amene kale anali ngati golide kwa ife,
tsopano akuŵayesa mbiya zadothi
zimene woumba amachita kuumba ndi manja ake.
3Ngakhale nkhandwe siziwumira bere,
zimayamwitsa ana.
Koma anthu anga ndi ankhalwe,
ali ngati nthiŵatiŵa zakunkhalango.
4Lilime la mwana wakhanda
limakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu.
Ana aang'ono amafuna chakudya,
koma palibe woŵapatsa mpang'ono pomwe.
5Amene ankadya zokoma akuthera m'miseu.
Amene ankavala zokongola zokhazokha
tsopano ali gone pa dzala.
6 Gen. 19.24 Chilango cha anthu anga nchachikulu kwambiri
kupambana chilango cha anthu a ku Sodomu,
amene adalangidwa pa kamphindi chabe,
ndipo panalibe wochitapo kanthu kuti aŵathandize.
7Akalonga ake anali oŵala koposa chisanu chambee,
oyera kuposa mkaka.
Matupi ao anali ofiira kupambana miyala ya rubi.
Anali ndi maonekedwe okongola ngati miyala ya safiro.
8Koma tsopano nkhope zao zasanduka zakuda ngati mwaye.
Palibe amene akuŵazindikira m'miseu.
Khungu lao lachita makwinyamakwinya,
langoti gwa ngati mtengo.
9Amene adaphedwa pa nkhondo anali amwai kwambiri
kupambana amene adafa ndi njala.
Ameneŵa ankafooka pang'onopang'ono mpaka kutsirizika,
chifukwa chosoŵa chakudya.
10 Deut. 28.57; Ezek. 5.10 Ngakhale akazi achifundo ndi manja ao omwe
adafika pophika ana ao.
Ana aowo adasanduka chakudya chao
pa nthaŵi imene anthu anga adaonongedwa.
11Chauta adakwiya kwambiri,
nagwetsa pansi mkwiyo wake wamotowo.
Adayatsa moto ku Ziyoni
ndipo motowo udaononga maziko a mzindawo.
12Mafumu a pa dziko lapansi sadakhulupirire,
kapena wina aliyense wokhala pa dziko lapansi,
kuti adani kapena ankhondo
nkuloŵa pa zipata za Yerusalemu.
13Zimenezi zidachitika
chifukwa cha machimo a aneneri ake
ndi ntchito zoipa za ansembe ake,
amene ankakhetsa magazi a anthu osalakwa
m'malinga amumzindamu.
14Ankangoyendayenda m'miseu ngati akhungu,
zovala zao zili magazi psu,
mwakuti palibe munthu woti nkuzikhudza.
15Anthu ankaŵafuulira kuti,
“Chokani, inu anthu oipitsidwa.
Chokani! Chokani apa! Musakhudzane ndi ife!”
Motero adathaŵa, namangoyendayenda,
anthu a mitundu ina ankati,
“Asadzakhalenso ndi ife.”
16Chauta mwiniwake ndiye adaŵamwaza,
salabadakonso za iwo.
Ansembe sadaŵalemekezenso.
Akuluakulu sadaŵamvere chifundo.
17Maso athu adatopa nkuyang'anira chithandizo,
koma popanda phindu.
Tidadikiradikira mtundu wina wa anthu
amene sangathe kutipulumutsa.
18Anthu ankangotilondola nthaŵi zonse,
kotero kuti sitinkathanso kuyenda m'miseu yathu.
Masiku athu ankacheperachepera,
imfa yathu idaayandikira,
ndithu chimalizo chinali chitafika.
19Anthu otilondolawo anali aliŵiro
kupambana adembo ouluka mu mlengalenga.
Adatipirikitsa ku mapiri,
adatilalira ku chipululu kuti atiphe.
20Wodzozedwa wa Chauta uja,
amene anali ngati mpweya wotipatsa moyo,
adakodwa m'misampha mwao.
Iyeyo amene tinkati adzatithandiza
ife okhala pakati pa anthu a mitundu ina.
21Kondwerani ndipo musangalale, inu anthu a ku Edomu,
inu anthu okhala m'dziko la Uzi.
Inunso chikho cha mavuto chidzakufikirani pa nthaŵi yanu.
Mudzaledzera mpaka kuvula zovala.
22Chilango cha machimo anu,
inu anthu a ku Ziyoni, chatheratu,
Chauta satalikitsa ukapolo wanu.
Koma inu anthu a ku Edomu,
Chauta adzakulangani chifukwa cha machimo anu.
Zolakwa zanu adzaziwulula poyera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.