1M'mbali mwa mitsinje ya ku Babiloni,
kumeneko tidakhala pansi
nkumalira tikukumbukira Ziyoni.
2Kumeneko tidapachika apangwe athu
pa mitengo ya misondodzi.
3Kumeneko anthu otigwira ukapolo adatipempha
kuti tiimbe nyimbo.
Otizunza adatipempha
kuti tisangalale,
adati,
“Tatiimbiraniko nyimbo ya ku Ziyoni.”
4Tsono ife tidati,
“Tingaimbe bwanji nyimbo ya Chauta
kuchilendo ngati kuno?”
5Ndikakuiŵala iwe Yerusalemu,
dzanja langa lamanja liwume.
6Lilime langa likangamire
ku mnakanaka m'kamwa mwanga,
ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu
ndi kukuwona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri.
7Kumbukirani, Inu Chauta,
zimene adachita Aedomu
pa tsiku lija la kuwonongeka kwa Yerusalemu,
muja ankati,
“Mgwetseni pansi, mgwetseni pansi,
mpaka pa maziko ake.”
8 Chiv. 18.6 Mzinda wa Babiloni, iwe woyenera kuwonongedwawe,
adzakhala wodala munthu amene adzakubwezera
zimene watichita ifezi.
9Adzakhala wodala munthu amene adzatenga makanda ako
ndi kuŵakankhanthitsa ku thanthwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.