Miy. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

M'mene nzeru imapezekera.

1Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa,

koma mtima wako usunge malamulo anga.

2Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka,

ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

3Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe,

makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi,

uŵalembe mumtima mwako.

4 Lk. 2.52 Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino

pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.

5Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse,

usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

6Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu,

choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

7 Aro. 12.16 Usamadziwona ngati wanzeru.

Uziwopa Chauta, ndipo uleke zoipa.

8Kuchita choncho kudzapatsa thupi lako moyo,

kudzalimbitsa mafupa ako.

9Uzilemekeza nacho Chauta chuma chako chonse,

uzimuyamika nazo zokolola zako zonse zam'minda.

10Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri,

mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo.

11 Yob. 5.17 Ahe. 12.5, 6 Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta,

usatope nako kudzudzula kwake.

12 Chiv. 3.19 Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda,

monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

13Ngwodala munthu amene wapeza nzeru,

amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

14pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva,

nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

15Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali.

Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.

16Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali.

Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu.

17Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo,

nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha.

18Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa.

Ngodala amene amaikangamira molimbika.

19Pamene adakhazikitsa dziko lapansi,

Chauta adaonetsa nzeru.

Pamene adakhazikitsa zakumwamba,

adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.

20Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko,

ndipo mitambo idagwetsa mvula,

adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu.

21Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni

usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino,

ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe.

22Zimenezi zidzakupatsa moyo,

moyo wake wokongola ngati mkanda wam'khosi.

23Tsono udzayenda pa njira yako mosaopa,

phazi lako silidzaphunthwa konse.

24Ukamakhala pansi, sudzachita mantha,

ukamagona, udzakhala ndi tulo tabwino.

25Usamaopa zoopsa zobwera modzidzimutsa,

usamachita mantha ndi tsoka lodzagwera anthu oipa.

26Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako,

adzasunga phazi lako kuti lingakodwe.

27 Mphu. 4.3 Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira,

pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho.

28Usamuuze mnzakoyo kuti,

“Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,”

pamene uli nazo tsopano lino.

29Usamkonzekere chiwembu mnzako,

amene amakhala nawe pafupi mokudalira.

30Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa

pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse.

31Usachite naye nsanje munthu wachiwawa,

usatsanzireko khalidwe lake lililonse.

32Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa,

koma olungama okha amayanjana nawo.

33Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa,

koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.

34 Yak. 4.6; 1Pet. 5.5 Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza,

koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima.

35Anthu anzeru adzalandira ulemu,

koma zitsiru adzazichititsa manyazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help