Yob. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Apo Bilidadi, Msuhi, adayankha Yobe kuti,

2“Kodi udzakhala ukulankhulabe zoterezi mpaka liti?

Mau akoŵa akungopita ngati mphepo.

3Kodi Mulungu amapotoza kuweruza kwake?

Kodi Mphambe amalephera kuchita zachilungamo?

4Kapena ana ako adamchimwira,

nkuwona Mulungu adaŵalanga chifukwa cha zochimwa zaozo.

5Ngati iwe uchita zimene Mulungu afuna,

ngati upemba kwa Mphambe,

6ngati ukhala wangwiro ndi wolungama,

ndithudi Mulungu adzachitapo kanthu, nkukuthandiza.

Adzakubwezera zabwino zonse ngati mphotho yokuyenerera.

7Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa,

kuyerekeza ndi m'mene udzakhalira komaliza.

8 Mphu. 8.9 “Tsono ndikukupempha

kuti ufunsefunse kwa anthu amvulazakale,

usinkhesinkhe zimene makolo athu adakumana nazo.

9Ife ndife adzulodzuloli,

sitidziŵa kanthu ai.

Moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.

10Kodi anthu amvulazakalewo nkupanda kukuphunzitsa?

Kodi iwo nkupanda kukuuza zinthu?

Pajatu mau a akulu akoma akagonera.

11“Kodi gumbwa nkumera pa nthaka yopanda chinyontho?

Nanga bango nkukondwa kumene kulibe madzi?

12Popanda madzi zimenezi zimafota

zikali zaziŵisi ndi zosadula,

zimauma msanga kupambana chomera china chilichonse.

13Ndimo m'mene zimaŵachitikira anthu oiŵala Mulungu.

Chikhulupiriro cha munthu wosapembedza Mulungu chimatha.

14Kulimba mtima kwake kumafooka,

zimene amakhulupirira zili ngati ukonde wa kangaude.

15Amatsamira pa nyumba yake,

koma nyumbayo si yolimba konse.

Amaigwiritsa, komabe siikhalitsa.

16Munthu woipayo ali ngati zomera

zokondwa ngakhale mpadzuŵa pomwe,

ndipo nthambi zake zimatambalala pa munda wake.

17Mizu yake imayanga pa miyala,

ndipo imakangamira pa thanthwe.

18Koma mutamchotsa pamalo pakepo,

palibe ndi mmodzi yemwe angadziŵe

kuti iyeyo anali pamenepo.

19Zokondwetsa zokhazo

ndizo zidzakhala phindu la ntchito zake,

kenaka ena adzabwera kudzaloŵa m'malo mwake.

20“Ndithu Mulungu sangamkane munthu wopanda cholakwa,

komanso anthu olakwa

Mulungu sangaŵathandize konse.

21Iye adzadzaza chiphwete m'kamwa mwako,

ndipo udzafuula mokondwa.

22Amene amadana nawe adzachita manyazi,

malo okhalako anthu oipa sadzaonekanso.”

Yobe

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help