1M'mamaŵa kutacha Yoswa adanyamuka. Iye, pamodzi ndi Aisraele onse, adatuluka ku Sitimu kuja, napita ku Yordani, ndipo adagona kumeneko.
2Patapita masiku atatu, atsogoleri adakayendera zithando zonse,
3namauza anthu kuti, “Mukadzaona ansembe Achilevi aja atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, mudzanyamuke pamalo panu ndi kuŵatsata.
4Potero mudzaidziŵa njira yoyenera kutsata, popeza kuti nkale lomwe kumeneko simudadzereko. Komatu tsono Bokosi lachipanganolo musaliyandikire. Pakati pa inu ndi Bokosilo pazikhala mtunda wosachepera kilomita imodzi.”
5Motero Yoswa adauza anthu onse kuti, “Mudzisungetu tsono, chifukwa maŵa Chauta adzachita zodabwitsa zazikulu pakati panu.”
6M'maŵa mwake Yoswa adauza ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chauta, muwoloke, mutsogolere anthuwo.” Iwowo adachitadi monga momwe Yoswa adanenera.
7Apo Chauta adauza Yoswa kuti, “Zimene ndikuchita lerozi, ndizo zidzapatse Aisraele onse mtima wokulemekeza iwe, kuti ndiwe munthu wamkulu. Ndipo adzadziŵa kuti Ine ndili nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose.
8Ansembe amene akunyamula Bokosi lachipangano la Chauta, uŵalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yordani, muloŵe m'madzimo ndi kuima m'mphepete.’ ”
9Tsono Yoswa adaŵauza anthuwo kuti, “Bwerani kuno, mudzamve zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani.
10Motero mudzadziŵa kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamapita patsogolo, Iye adzapirikitsa Akanani onse, pamodzi ndi Ahiti, Ahivi, Aperizi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.
11Pamenepo Bokosi lachipangano la Chauta wa dziko lonse lapansi liwoloke Yordani patsogolo panu.
12Tsopano musankhe amuna khumi ndi aŵiri kuchokera ku fuko lililonse la Aisraele.
13Ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi, akangoponda madziwo, madzi onse a Yordani ochokera kumtunda adzaleka kuyenda, ndipo adzaima ngati chipupa.”
14Nyengo imeneyo inali ya kholola, ndipo mtsinje unali wodzaza kwambiri. Anthu onse adachoka ku zithando kukaoloka mtsinje wa Yordani uja. Ansembe ndiwo anali patsogolo, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta lija.
15Pamene ansembewo adafika pa chibumi cha Yordani, natsikira m'madzimo ndi kuponda madziwo,
16madzi onse adaima osayendanso. Madzi akumtunda adaundana ngati khoma lalitali, kuchokera ku Adama mpaka ku mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja Yakufa, adatheratu pamalopo, ndipo anthu adaolokera tsidya lina, pafupi ndi Yeriko.
17Chonsecho nkuti ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja ataima pakatimpakati pa mtsinje wa Yordani uja, mpaka anthu onse adatha kuwoloka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.