1 Sam. 28 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraele.

1Nthaŵi ina Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo, kuti amenyane ndi Aisraele. Tsono Akisi adauza Davide kuti, “Udziŵe kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita nane ku nkhondo.”

2Davide adayankha kuti, “Chabwino, mudzaona zimene ndichite ine mtumiki wanu.” Akisi adati, “Chabwino, ndidzakuika kuti ukhale mlonda wonditchinjiriza pa moyo wako wonse.”

Saulo apempha nzeru kwa oombedza.

3 1Sam. 25.1 Lev. 20.27; Deut. 18.10, 11 Nthaŵi imeneyi nkuti Samuele atafa, ndipo Aisraele atalira maliro ake, namuika ku mzinda wake ku Rama. Saulo anali atachotsa anthu onse olankhula ndi mizimu ndi anthu onse oombeza maula am'dzikomo.

4Tsono Afilisti adasonkhana nadzamanga zithando zao zankhondo ku Sunemu. Saulo nayenso adasonkhanitsa Aisraele, ndipo adamanga zithando ku Gilibowa.

5Saulo ataona gulu laankhondo la Afilisti, adayamba kuwopa ndi kunjenjemera kwambiri.

6Num. 27.21 Adapempha nzeru kwa Chauta, koma sadamuyankhe ngakhale podzera m'maloto, kapena mwa Urimu kapena mwa aneneri.

7Pamenepo Saulo adauza nduna zake kuti, “Mundifunire mkazi wolankhula ndi mizimu kuti ndipite kwa iyeyo, ndikapemphe nzeru.” Ndunazo zidamuuza kuti, “Ku Endori aliko mkazi wolankhula ndi mizimu.”

8Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.”

9Mkaziyo adati, “Inutu mukudziŵa zimene adachita mfumu Saulo. Suja adachotsa m'dziko muno anthu olankhula ndi mizimu ndiponso oombeza? Chifukwa chiyani tsono mukunditchera msampha kuti mundiphe?”

10Koma Saulo adalonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Chauta wamoyo, sudzalangidwa kaamba ka zimenezi.”

11Mphu. 46.20Apo mkaziyo adafunsa kuti, “Kodi ndikuitanireni yani?” Saulo adati, “Itanire Samuele.”

12Pamene mkaziyo adaona Samuele, adakuwa kwambiri nati, “Chifukwa chiyani mwandinyenga? Ndinu mfumu Saulo!”

13Tsono mfumuyo idamuuza kuti, “Usaope. Kodi ukuwona chiyani?” Mkaziyo adati, “Ndikuwona mzimu ukutuluka pansi.”

14Saulo adafunsa mkaziyo kuti, “Kodi maonekedwe a mzimuwo ngotani?” Mkaziyo adati, “Imene ikutuluka ndi nkhalamba, yavala mkanjo.” Apo Saulo adadziŵa kuti ndi Samuele ameneyo, ndipo adapereka ulemu pakuŵerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi.

15Pamenepo Samuele adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani wandivuta ponditulutsa kuti ndibwere kuno?” Saulo adayankha kuti, “Ndavutika kwambiri, pakuti Afilisti abwera kudzandithira nkhondo, ndipo Mulungu wandifulatira osandiyankhanso, ngakhale podzera mwa aneneri, kapena m'maloto. Nchifukwa chake ndakuitanani kuti mundiwuze zomwe ndiyenera kuchita.”

16Samuele adati, “Chifukwa chiyani ukufuna ine tsopano, chikhalirecho Chauta wakufulatira kale ndipo wasanduka mdani wako?

171Sam. 15.28 Chauta wakuchita zomwe adakuuza kudzera mwa ine. Wakulanda ufumu, waupereka kwa wina, kwa Davide.

181Sam. 15.3-9 Chauta akuchita zimenezi lero, chifukwa chakuti sudamvere mau ake, ndipo sudaonongeretu Aamaleke ndi zinthu zao.

19Tsono adzakupereka iweyo pamodzi ndi Aisraele kwa Afilisti. Ndipo maŵa, iwe ndi ana ako, mudzabwera kuli ine kuno. Ndithudi, Chauta adzapereka gulu lankhondo la Aisraele kwa Afilisti.”

20Pompo Saulo adagwa pansi, kuchita kuti nyutu, ali wodzazidwa ndi mantha chifukwa cha mau a Samuele. Ndipo analibenso nyonga, poti sadadye kanthu tsiku lonse.

21Apo mkazi uja adasendera pafupi ndi Saulo, ndipo ataona kuti akuchita mantha, adamuuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ine ndataya moyo wanga pomvera zimene munandiwuza.

22Nchifukwa chake tsono, inunso mumvere mau anga. Mundilole ndikuikireni kabuledi pang'ono, mudye kuti muwone nyonga zoyendera.”

23Saulo adakana nati, “Ine sindidya ai.” Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo adamkakamiza, ndipo adaŵamvera. Choncho adadzuka pansi paja nakhala pa bedi.

24Mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa, ndipo adamupha mwachangu. Adatenga ufa naukanyanga, naphika buledi wosatupitsidwa.

25Tsono adadzapereka bulediyo kwa Saulo ndi nduna zake, ndipo onse adadya. Pambuyo pake adanyamuka, nachokapo usiku womwewo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help