Ahe. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za m'mene tingakondweretsere Mulungu

1Pitirizani kukondana monga abale.

2Gen. 18.1-8; 19.1-3; Tob. 5.4, 5 Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.

3Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi.

4 Lun. 3.13 Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.

5 Deut. 31.6, 8; Yos. 1.5 Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

6Mas. 118.6 Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti,

“Ambuye ndiwo Mthandizi wanga,

sindidzachita mantha.

Munthu angandichite chiyani?”

7Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.

8Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi mpaka muyaya.

9Musalole zophunzitsa zosiyanasiyana ndiponso zachilendo kuti zikusokeretseni. Choyenera kutilimbitsa mtima ndi kukoma mtima kwa Mulungu, osati malamulo onena za chakudya ai. Malamulo ameneŵa sadaŵapindulitsepo anthu amene ankaŵatsata.

10Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo.

11Lev. 16.27 Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa.

12Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.

13Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi.

14Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza.

15Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.

16Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.

17Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

18Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo.

19Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga.

Pemphero

20Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya.

21Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.

Mau otsiriza

22Ndikukupemphani, inu abale anga, kuti muŵalandire bwino mau okulimbitsani mtimaŵa, pakuti ndangokulemberani mwachidule.

23Ndikufuna kuti mudziŵe kuti Timoteo, mbale wathu, amtulutsa m'ndende. Akafika msanga, ndidzabwera naye kwanuko podzakuwonani.

24Mutiperekereko moni kwa atsogoleri anu onse, ndi kwa anthu onse a Mulungu. Abale a ku Italiya akuti moni.

25Mulungu akukomereni mtima nonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help