Ntc. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Barnabasi ndi Saulo atumidwa

1Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo.

2Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”

3Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.

Za ku Kipro

4Barnabasi ndi Saulo, otumidwa ndi Mzimu Woyera aja, adapita ku Seleukiya. Kuchokera kumeneko adayenda m'chombo nakafika ku chilumba cha Kipro.

5Atafika ku mzinda wa Salami, adalalika mau a Mulungu m'nyumba zamapemphero za Ayuda. Analinso ndi Yohane womaŵathandiza.

6Iwo adabzola chilumba chonse mpaka kukafika ku mzinda wa Pafosi. Kumeneko adapezako munthu wina wamasenga, dzina lake Barayesu, Myuda amene ankadziyesa mneneri.

7Iyeyu ankakhala kwa bwanamkubwa Sergio Paulo, munthu wanzeru. Sergio Pauloyo adaitana Barnabasi ndi Saulo, chifukwa iye ankafunitsitsa kumva mau a Mulungu.

8Koma kumeneko adapezanako ndi Elimasi, wamasenga uja (Elimasi ndiye kuti Wamasenga). Iyeyo adatengana nawo, kuwopa kuti bwanamkubwa uja angakhulupirire.

9Koma Saulo, amene ankatchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adampenyetsetsa

10nati, “Iwe mwana wa Satana, mdani wa chilungamo, wa mtima wa kunyenga kulikonse ndi kuchenjeretsa kwamtundumtundu, udzaleka liti kupotoza njira zolungama za Ambuye?

11Ona dzanja la Ambuye likukantha tsopano apa. Ukhala wakhungu osaonanso dzuŵa pa kanthaŵi.” Nthaŵi yomweyo khungu ndi mdima zidamgweradi, ndipo adayamba kufunafuna anthu oti amgwire dzanja ndi kumtsogolera.

12Pamene bwanamkubwa uja adaona zimene zidachitikazo, adakhulupirira. Adaadabwa nazo zimene iwo adaaphunzitsa za Ambuye.

Za ku Antiokeya m'dera la Pisidiya

13Paulo ndi anzake adayenda m'chombo kuchokera ku Pafosi kukafika ku Perga m'dera la Pamfiliya. Koma Yohane adaŵasiya nabwerera ku Yerusalemu.

14Kuchokera ku Perga iwo adapitirira nakafika ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapempherero ya Ayuda, nakhala pansi.

15Ataŵerengedwa mau a m'buku la Malamulo a Mose ndi m'buku la aneneri, akulu a nyumba yamapemphero ija adaŵatumira mau oŵauza kuti, “Abale, ngati muli ndi mau olimbikitsa nawo anthuŵa, nenani.”

16Apo Paulo adaimirira nakweza dzanja kuti anthu akhale chete, ndipo adayamba kulankhula. Adati,

“Inu Aisraele, ndi ena nonse oopa Mulungu, mverani.

17 adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Aŵiriŵa adalankhula ndi anthu aja, naŵapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adaŵachitira mwa kukoma mtima kwake.

44Pa tsiku la Sabata linalo pafupi anthu onse amumzindamo adasonkhana kuti amve mau a Ambuye.

45Pamene Ayuda aja adaona anthu ambiriwo, adachita nsanje kwambiri. Adayamba kutsutsa zimene Paulo ankanena, ndipo adamchita chipongwe.

46Koma Paulo ndi Barnabasi adalankhula molimbika, adati, “Kudaayenera ndithu kuti tiyambe talalika mau a Mulungu kwa inu. Tsono popeza kuti mwaŵakana, ndipo potero mwaonetsa nokha kuti ndinu osayenera kulandira moyo wosatha, ife tikusiyani, tipita kwa anthu akunja.

47Yes. 42.6; 49.6 Paja Ambuye adatilamula kuti,

“ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja,

kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”

48Pamene anthu a mitundu ina aja adamva zimenezi, adakondwa, nayamikira wawu a Ambuye. Ndipo onse amene Mulungu adaaŵasankha kuti alandira moyo wosatha, adakhulupirira.

49Mau a Ambuye adafalikira m'dziko monse muja.

50Koma Ayuda aja adautsa mitima ya akazi ena apamwamba opembedza Mulungu, ndiponso ya atsogoleri achimuna amumzindamo. Tsono adayambitsa mazunzo osautsa Paulo ndi Barnabasi, naŵapirikitsa m'dziko mwaomo.

51Mt. 10.14; Mk. 6.11; Lk. 9.5; 10.11Koma iwo adasansa fumbi la kumapazi kwao moŵatsutsa, napita ku Ikonio.

52Ndipo ophunzira a ku Antiokeya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo adakhala ndi chimwemwe chachikulu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help