1Pakutha pa zaka 480 Aisraele atatuluka ku Ejipito, chaka chachinai cha ufumu wa Solomoni wolamulira Aisraele, pa mwezi wa Zivi, umene uli mwezi wachiŵiri, Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta.
2Nyumba imene mfumu Solomoni adamangira Chauta muutali mwake inali ya mamita 27, muufupi mwake inali ya mamita asanu ndi anai, ndipo msinkhu wake unali wa mamita pafupi 13 ndi theka.
3Tsono chipinda chakubwalo m'mimba mwake munali mwa mamita asanu ndi anai, kulingana ndi muufupi mwa Nyumbayo. Kutalika kunali kwa mamita anai ndi theka.
4Adaika mawindo amene mafuremu ake anali oloŵa m'kati mwa makoma.
5Adamanganso zipinda zosanjikizana pafupi ndi khoma la Nyumba, kuzungulira makoma a Nyumba yaikuluyo ndi a malo opatulika a m'kati.
6Chipinda chapansi m'mimba mwake chinali ngati mamita aŵiri, ndipo chipinda chapakati m'mimba mwake chinali ngati mamita aŵiri ndi theka. Chipinda cha pamwamba penipeni m'mimba mwake chinali mamita atatu. Kunja, pa makomawo adamangapo nsolomondo kuzungulira Nyumbayo, kuti asamapise mitanda m'makoma a Nyumbayo.
7Nyumbayo poimanga, idamangidwa ndi miyala yosemeratu. Choncho pogwira ntchitoyo, sipadamveke nyundo, nkhwangwa kapena chipangizo chilichonse chachitsulo.
8Chipata choloŵera ku chipinda chapansi chija chinali chakumwera kwa Nyumbayo. Anthu ankachita kukwera makwerero pochoka ku chipinda chapansi kupita ku chipinda chapakati, chimodzimodzi pochoka ku chipinda chapakati kupita ku chipinda chapamwamba.
9Choncho adamanga Nyumbayo mpaka kuimaliza. Ndipo siling'i yake ya Nyumbayo adaipanga ndi mitanda ndi matabwa amkungudza.
10Adatsirizanso zipinda zosanjikana kuzungulira Nyumbayo. Chipinda chilichonse msinkhu wake unali ngati mamita aŵiri, ndipo adazilumikiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza.
11Tsono Chauta adauza Solomoni kuti,
12“Kunena za Nyumba ukumangayi, iwe ukamamvera mau anga ndi malangizo anga ndi kutsata malamulo anga onse, Ine ndidzakuchitiradi zimene ndidalonjeza kwa Davide bambo wako.
13Ndiye kuti Ine ndidzakhala pakati pa Aisraele, Aisraele anthu anga sindidzaŵasiya.”
14Choncho Solomoni adamanga Nyumba ya Chauta naimaliza.
Zokongoletsa za m'kati mwa Nyumba ya Chauta(2 Mbi. 3.8-14)15Pambuyo pake makoma a Nyumba ya Chauta m'kati mwake Solomoni adaŵachinga ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku siling'i. Pansi pake pa Nyumbayo adayalapo matabwa apaini.
16Eks. 26.33, 34 Kumbuyo kwa Nyumbayo adadula chipinda kutalika kwake mamita asanu ndi anai. Adachimanga ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i. Chipindachi adachimanga m'kati mwa Nyumbayo, kuti chikhale chipinda chopatulika cham'kati, malo opatulika kopambana.
17Chigawo cha Nyumba chimene chinali patsogolo pa chipinda chopatulikacho, m'litali mwake chinali mamita 18.
18M'kati mwa Nyumbayo pa matabwa amkungudza aja adajambulapo zithunzi za zikho ndi za maluŵa. Ponse panali mkungudza wokhawokha, miyala ya khoma osaoneka.
19Chipinda chopatulika chija adachikonza m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, kuti aikemo Bokosi lachipangano la Chauta.
20Chinali cha mamita asanu ndi anai ponseponse, m'litali mwake, m'mimba mwake ndiponso mumsinkhu mwake. Ndipo adachikuta ndi golide weniweni. Adapanganso guwa lansembe la matabwa amkungudza.
21Tsono Solomoni adakuta golide weniweni m'kati mwake mwa Nyumbayo, ndipo adalambalika maunyolo agolide mopingasitsa kutsogolo kwa chipinda chopatulika cham'kati naŵakuta ndi golide. Chipinda chimenechinso chidakutidwa ndi golide.
22Eks. 30.1-3 Motero adaikuta Nyumba yonseyo ndi golide mpaka idatha. Guwa lansembe la m'chipinda chopatulika nalonso adalikuta ndi golide.
23 Eks. 25.18-20 Adapanga akerubi aŵiri a mtengo wa olivi, msinkhu wa aliyense unali mamita anai ndi theka, ndipo adaŵaika m'chipinda chopatulika cham'kati chija.
24Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, phiko linanso kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu. Kufunyulula mapiko aŵiriwo, kuchokera nsonga ina mpaka nsonga ina, kutalika kwake kunali mamita anai ndi theka.
25Kerubi winayo msinkhu wake unalinso mamita anai ndi theka. Akerubi aŵiri onsewo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanananso.
26Kerubi mmodzi msinkhu wake unali mamita anai ndi theka, kerubi winayo analinso chimodzimodzi.
27Solomoni adaika akerubiwo m'chipinda cha m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo. Ndipo mapiko ao adaŵatambalitsa kotero kuti phiko limodzi la kerubi mmodzi linkakhudza khoma lina, ndipo phiko limodzinso la kerubi winayo linkakhudza khoma lina. Mapiko enawo ankakhudzana pakati pa Nyumba.
28Ndipo akerubiwo adaŵakuta ndi golide.
29Adazokota zithunzi za akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa, kuzungulira makoma onse a Nyumbayo, ndiponso m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe.
30Kenaka adayalanso golide pansi m'Nyumbamo m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe.
31Ndipo adapanga zitseko za mtengo wa olivi zoloŵera ku chipinda chopatulika chija. Lentulo pamodzi ndi mphuthu zake zinali ndi mbali zisanu.
32Pa zitseko ziŵiri zija za mtengo wa olivi adazokotapo zithunzi za akerubi, za mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa. Tsono zitsekozo adazikuta ndi golide, ndipo adapaka golide pa akerubiwo ndi pa mitengo ya mgwalangwa ija.
33Adapanganso chimodzimodzi mphuthu za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo, zokhala ndi mbali zinai.
34Ndipo adapanga zitseko ziŵiri za mtengo wa paini. Zigawo ziŵiri za chitseko chimodzi zinali zotha kupindapinda, zigawo ziŵiri za chitseko china zinalinso zotha kupindapinda.
35Pa zitsekopo adazokotapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndiponso maluŵa. Ndipo zozokotazo adazikuta ndi golide wopsapsalala.
36Adamanganso bwalo lam'kati. Makoma ake adapanga ndi miyala yosema mizere itatu, mosinthanitsana ndi mzere umodzi wa matabwa amkungudza.
37Maziko a Nyumba ya Chauta adamangidwa pa chaka chachinai, mwezi wa Zivi.
38Tsono pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumbayo adatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Nyumbayo adaimanga pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.