2 Sam. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kupambana kwa Davide pa nkhondo.(1 Mbi. 18.1-17)

1Pambuyo pake Davide adathira nkhondo Afilisti, naŵagonjetsa, ndipo adaŵalanda mzinda wa Metegama.

2Kenaka Davide adagonjetsa Amowabu. Adalamula onsewo kuti agone pansi m'mizere itatu pa gulu lililonse. Pagulu lililonse anali kupha anthu amene anali pa mizere iŵiri yoyamba, kusiyapo a mzere wachitatu. Choncho Amowabu adasanduka akapolo a Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye.

3Davide adagonjetsanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pamene Hadadezereyo ankapita kumtunda kwa mtsinje wa Yufurate, kuti akakhazikitsenso ulamuliro wake ku deralo.

4Davide adagwira ankhondo a Hadadezere. Okwera pa akavalo analipo 1,700, a pansi analipo 20,000. Ndipo adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okakoka magaleta, koma adasungako ena a magaleta 100.

5Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000.

6Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko, m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita.

7Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu.

8Kuchokera ku Beta ndi ku Berotai, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri.

9Pamene Toi mfumu ya ku Hamati adamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezere,

10adatuma mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Toi kaŵirikaŵiri. Tsono Yoramuyo adabwera ndi mphatso zopangidwa ndi siliva, golide, ndi mkuŵa.

11Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina amene adaŵagonjetsa.

12Anthuwo anali Aedomu, Amowabu, Aamoni, Afilisti ndi Aamaleke. Zina zinali zimene adaafunkha kwa Hadadezere mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba.

13 Mas. 60 Mbiri ya Davide idamveka ponseponse. Pamene ankabwerera, anali atapha Aedomu 18,000 ku chigwa cha Mchere.

14Tsono adaika zigono za ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu. Mu Edomu monse munali timagulu ta ankhondo, choncho Aedomu onse adasanduka otumikira Davide. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.

15Motero Davide adalamulira dziko lonse la Israele, ndipo ankayendetsa zonse mwachilungamo ndi mosakondera.

16Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri.

17Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Seraya anali mlembi.

18Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali ansembe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help