1Pambuyo pake Davide adasonkhanitsa anthu amene anali naye kuti aŵagaŵe m'magulu, ndipo adaŵaikira atsogoleri, ena olamulira anthu zikwi, ena olamulira anthu mazana.
2Ndipo Davide adatumiza gulu lankhondo ataligaŵa patatu, chigawo chimodzi cholamulidwa ndi Yowabu, china cholamulidwa ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mng'ono wake wa Yowabu, china cholamulidwa ndi Itai Mgiti. Tsono mfumu idauza anthuwo kuti, “Inenso ndipita nao.”
3Koma anthuwo adati, “Inuyo simupita nao, chifukwa ife tikathaŵa, adani sadzatisamala. Ngati theka la ife lifa, iwo sadzasamalako za ife. Koma inu mukuposa anthu 10,000 mwa ife. Nchifukwa chake nkwabwino kwambiri kuti inu muzingotitumizira chithandizo kuchokera kumzindako.”
4Mfumu idaŵauza kuti, “Chilichonse chimene chikukomereni, ndidzachita.” Choncho mfumuyo idakaimirira pambali pa chipata nthaŵi imene gulu lonse lankhondo linkatuluka mazanamazana, ndiponso zikwizikwi.
5Ndipo mfumu idalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumlezere mtima mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.” Anthu onse adamva pamene mfumu inkalamula atsogoleri a ankhondo kunena za Abisalomu.
6Tsono ankhondo adatuluka kunka ku thengo kukamenyana ndi Aisraele. Ndipo nkhondo idachitikira ku nkhalango ya Efuremu.
7Aisraele adagonjetsedwa kumeneko ndi ankhondo a Davide. Motero tsiku limenelo adaphedwa anthu ambiri okwanira 20,000 onse pamodzi.
8Nkhondo idafalikira m'dziko lonselo, ndipo zoopsa zam'nkhalango zidapha anthu ambiri kuposa anthu ophedwa ndi lupanga.
9Mwadzidzidzi Abisalomu adakumana ndi ankhondo a Davide. Abisalomuyo anali atakwera pa bulu wake, ndipo buluyo adaloŵa kunsi kwa nthambi zochindikira za mtengo wa thundu. Pamenepo Abisalomu adatsalira ali lendee, mutu wake utapanika pa nthambiyo, pamene bulu ankakwerayo adapitirira.
10Munthu wina ataona zimenezo, adauza Yowabu kuti, “Ndamuwona Abisalomu ali lendee mu mtengo wa thundu.”
11Yowabu adafunsa munthuyo kuti, “Nanga bwanji sudamphere pomwepo? Ndikadakondwa ndipo ndikadakupatsa ndalama zasiliva khumi ndiponso lamba.”
12Koma munthuyo adauza Yowabu kuti, “Ngakhale ndikadalandira m'manja mwangamu ndalama zasiliva zokwanira 1,000, sindikadasamula dzanja langa kuti ndiphe mwana wa mfumu. Paja mfumu idakulamulani inu ndi Abisai ndi Itai, ife tilikumva, kuti, ‘Mumtchinjirize mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.’
13Bwenzi nditanyoza mau a mfumuwo, pomupha mwana wake, ndipo zikadadziŵika, poti palibe kanthu kobisika pamaso pa mfumu, ndipo inu nomwe simukadanditeteza.”
14Apo Yowabu adati, “Ukunditayitsa nthaŵi!” Ndipo adatenga mikondo itatu m'manja mwake, nakabaya Abisalomu m'chifuŵa asanafe, akali lendee mu mtengo wa thunduwo.
15Pomwepo ankhondo khumi onyamula zida zankhondo za Yowabu, adazinga Abisalomu, namkantha mpaka kumupha.
16Pambuyo pake Yowabu adaliza lipenga loletsa nkhondo, ndipo ankhondo ake adabwerako kumene ankalondola Aisraele kuja.
17Ndipo ankhondowo adatenga mtembo wa Abisalomu, nakautaya m'chidzenje chachikulu m'nkhalango, naunjika mulu wa miyala padzenjepo. Aisraele onse adathaŵa, aliyense kuthaŵira kwao.
18Abisalomu akadali moyo, adaadzimangira chipilala m'chigwa cha mfumu, poti ankati, “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti adzakhale chikumbutso cha dzina langa.” Adaatchula chipilalacho dzina lake lomwe, ndipo mpaka pano chikutchulidwa kuti chikumbutso cha Abisalomu.
19Tsono Ahimaazi, mwana wa Zadoki, adati, “Imani ndithamange ndikauze mfumu nkhani yokondwetsayi yakuti Chauta waipulumutsa mfumuyo kwa adani ake.”
20Yowabu adauza Ahimaaziyo kuti, “Iwe usakanene zimenezi lero. Ukanene zimenezi tsiku lina, koma lero usakanene mbiri iliyonse, chifukwa mwana wa mfumu waphedwa.”
21Pambuyo pake Yowabu adauza Mkusi kuti, “Pita, ukauze mfumu zimene waziwonazi.” Mkusiyo adaŵeramira Yowabu mwaulemu, nayamba kuthamanga.
22Zitatero, Ahimaazi uja, mwana wa Zadoki, adauzanso Yowabu kuti, “Zitanizitani, mundilole kuti inenso ndimthamangire Mkusi uja.” Yowabu adamufunsa kuti, “Mwana wanga, chifukwa chiyani ukuti uthamange, pamene sudzalandirapo mphotho chifukwa cha uthenga umenewo?”
23Ahimaazi adati, “Zitanizitani, ine ndithamanga ndithu.” Apo Yowabu adamuuza kuti, “Chabwino, pita.” Choncho Ahimaazi adathamanga, kudzera njira yakuchigwa, nkumubzola Mkusi uja.
24Nthaŵi imeneyo nkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziŵiri, chakubwalo ndi cham'kati. Mlonda adakwera pa khoma nakaimirira pa denga la chipata. Adati atayang'ana, adaona munthu akuthamanga yekhayekha.
25Ndipo mlondayo adafuula nauza mfumu. Mfumuyo idati, “Ngati ali yekhayekha, ndiye kuti ali ndi nkhani yabwino.” Tsono munthu uja adafika ndithu, nayandikira pafupi.
26Mlondayo adaona munthu winanso akuthamanga. Ndipo adafuulira munthu wapachipata nati, “Onani, pali munthu winanso akuthamanga yekhayekha.” Apo mfumu idati, “Iyeyonso akubwera ndi nkhani yabwino.”
27Mlonda uja adati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi m'mene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu idati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”
28Tsono Ahimaazi adafuula kwa mfumu, kuti, “Nkwabwino!” Atatero adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu, nati, “Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wapereka m'manja mwanu anthu amene adaaukira inu mbuyanga mfumu.”
29Mfumu idamufunsa kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu, zinthu zamuyendera bwino?” Ahimaazi adauza mfumu kuti, “Pamene Yowabu amandituma ine, kapolo wanu, ndinaona chipiringu chachikulu cha anthu, sindikudziŵa kaya kwagwa zotani.”
30Pompo mfumu idati, “Patuka, kaime apo.” Iye adapatuka nakaima potero.
31Mkusi uja nayenso adafika, ndipo adati, “Ndakutengerani uthenga wabwino, mbuyanga mfumu. Lero lino Chauta wakupulumutsani ku mphamvu za anthu onse amene ankakuukirani.”
32Tsono mfumuyo idafunsa Mkusi uja kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu zinthu zamuyendera bwino?” Mkusiyo adayankha kuti, “Adani anu mbuyanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuukirani, ziŵaonekere zomwe zamuwonekera mwanayo.”
33Pamenepo mfumu idagwidwa ndi chisoni chachikulu, nikwera ku chipinda cham'mwamba pa chipata kukalira. Tsono popita inkati, “Iwe mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu. Kalanga ine, achikhala ndidaafa ndine m'malo mwako! Iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.