Esr. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hamani aphedwa

1Tsono mfumu idapita limodzi ndi Hamani ku phwando limene mfumukazi Estere adaakonza.

2Pa tsiku lachiŵiri la phwando, pamene ankamwa vinyo, mfumu idamufunsanso Estere kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ukupempha nchiyani? Chopempha chakocho ndidzakupatsa. Tsono chomwe ukufuna nchiyani? Ngakhale likhale hafu la ufumu wanga, ndidzakupatsa ndithu.”

3Apo mfumukazi Estere adayankha kuti, “Ngati ndakukomerani m'maso ndipo ngati chingakukondweretseni inu amfumu, mundisungire moyo wanga ndiponso musunge moyo wa anthu a mtundu wanga. Pempho langa ndi limeneli.

4Pajatu atigulitsa, ineyo ndi anthu a mtundu wanga, kuti tiwonongedwe, kuti atiphe, ndi kuti atifafaniziretu. Akadangotigulitsa kuti tikhale akapolo, amuna ndi akazi omwe, bwenzi nditakhala chete osalankhulapo kanthu, pakuti masautso athu sakadakhala oti inu amfumu nkuvutika nawo.”

5Tsono mfumu Ahasuwero adafunsa mfumukazi Estere kuti, “Kodi ndiye yaninso amene adakonzekera kuchita zimenezi? Ndipo ali kuti?”

6Estere adayankha kuti, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Uyu, Hamani woipa mtimayu!” Pamenepo Hamani adagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi.

7Tsono mfumu idanyamuka pa phwando itakwiya kwambiri, nipita ku munda wa ku nyumba yaufumu. Koma Hamani adatsala kuti apemphe mfumukazi Estere kuti apulumutse moyo wake. Adaadziŵa kuti mfumu yatsimikiza za kumchita choipa.

8Mfumu itabwerako ku munda wa ku nyumba yaufumu uja, poloŵa m'chipinda chomwera vinyo chija, idapeza Hamani atadzigwetsa pabedi pomwe panali Estere, pofuna kupempha chifundo. Apo mfumu idati, “Ha! Munthu ameneyu azikakamiza mfumukazi kuti achite naye zoipa m'nyumba mwanga muno, ine ndili pomwepo!” Mfumu itangotsiriza mau ameneŵa, anthu adamuphimba Hamani kumaso.

9Tsono Haribona, mmodzi mwa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu, adati, “Kuwonjezera pamenepo, Hamaniyu adakonza mtengo, kutalika kwake mamita 23, woti ati apachikepo Mordekai, munthu amene adakupulumutsani inu amfumu ndi mau ake. Moti mtengowo wauyedzeka kunyumba kwake.”

10Apo mfumu idati, “Kampachikeni pamenepo iyeyu.” Choncho anthuwo adampachika Hamani pa mtengo womwe mwiniwakeyo adaakonza kuti apachikepo Mordekai. Pambuyo pake mkwiyo wa mfumu udatsika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help