1Ndikamaitana,
mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga.
Mudabwera kudzandithandiza
pamene ndinali m'mavuto.
Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.
2Anthu inu, mudzaleka liti kunyoza ulemu wanga?
Bwanji mukukondabe zinthu zachabechabe?
Bwanji mukulakalakabe zinthu zonama?
3Koma tsono mudziŵe
kuti Chauta wadzipatulira Iye yemwe anthu olungama.
Chauta amamva ndikamuitana.
4 Aef. 4.26 Opani Mulungu, ndipo musachimwe.
Mukhale phee ndipo muganize zimenezi mu mtima
pamene mukugona.
5Perekani nsembe zanu ndi mtima wolungama,
ikani mitima yanu pa Chauta.
6Alipo ambiri amene amati,
“Ndani angatiwonetse zabwino?
Mutiyang'ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.”
7Koma Inu mwandisangalatsa mtima kwambiri,
kupambana anthu a zakudya ndi zakumwa zambiri!
8Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
pakuti Inu nokha Chauta
ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.