Lun. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Moyo wa anthu osamvera Mulungu

1Anthu osamvera Mulungu amaganiza molakwa kuti,

“Moyo wathu ndi wochepa

ndiponso womvetsa chisoni.”

Nthaŵi ya imfa ikafika,

palibe mankhwala oti nkumupulumutsa munthu.

Monga tikudziŵira, palibe ndi mmodzi yemwe

amene adabwerako ku dziko la akufa.

2Tidangobadwa mosayembekezeka,

pambuyo pake tidzangoti zii,

monga ngati sitidakhale konse ndi moyo.

Mpweya wa m'mphuno mwathu uli ngati utsi,

nzeru zathu zili ngati mbaliŵali ya moto,

yofumira mu mtima wathu pamene ukugunda.

3Mbaliŵaliyo itazima,

thupi lathu lidzasanduka ngati phulusa,

mpweya wathu udzazimirira ngati nkhungu.

4Kanthaŵi pang'ono ndipo dzina lathu

lidzaiŵalika,

palibe amene adzakumbukire zimene tidachita.

Moyo wathu udzapita ngati mtambo wouluzika,

udzatha ngati nkhungu

yomwazikana nkuŵala kwa dzuŵa,

yozimirira nkutentha kwa dzuŵalo.

5Nthaŵi yathu yokhala pansi pano

ili ngati mthunzi wongodutsa.

Tikafa tapita chonse,

chifukwa pamanda pamakhala pokhoma,

ndiye palibe amene amabwerako.

6 Yes. 22.13; 1Ako. 15.32 Anthu osamvera aja amati,

“Tiyeni tsono tikondwerere zabwino zoterezi,

tilidyere dziko ndi kukhutiratu

monga tinkachitira nthaŵi yaunyamata.

7Timwe vinyo wokoma mpaka kuledzera,

tidzole zonunkhira zamtengowapatali.

Tisaleke kukondwerera maluŵa

a nthaŵi yachilimwe.

8Tivale nsangamutu za mphundu za maluŵa

zisanafote.

9Wina aliyense mwa ife asalephere

kufika ku madyerero athu.

Tisiye zizindikiro za chisangalalo ponseponse,

chifukwa chimenechi ndiye chigawo chathuchathu

chokhalira ifeyo.

10“Munthu wolungama amene alibe chuma,

tiyeni timuzunze.

Mkazi wamasiye tisamuchitire chifundo,

munthu wokalamba, imvi zili mbu,

tisamulemekeze.

11Kwa ifeyo kuti tikhale achilungamo,

koma tiwonetse mphamvu zathu,

pakuti amene alibe mphamvu

ndiye kuti ngwopanda ntchito.

12Tsono timukhalizire munthu wolungama,

popeza kuti amativutitsa,

ndipo amatsutsana ndi ntchito zathu.

Amatidzudzula chifukwa chopandukira malamulo,

amatinena kuti timanyoza mwambo.

13Iye akuti ati amadziŵa Mulungu,

ndipo amadzitchula mwana wa Ambuye.

14Tikamuwona timamva kudzudzulidwa

m'maganizo mwathu,

tikangomuti tha,

ife pomwepo khwinya.

15Iye uja makhalidwe ake safanafana

ndi a anthu ena,

machitidwe ake ndi amtundu.

16Amatiyesa ife anthu onyozeka,

amapewa machitidwe athu

ngati zinthu zonyansa.

Amaganiza kuti imfa ya munthu wolungama

ndi yodalitsidwa,

amanyadira kuti Mulungu ndi atate ake.

17Tiyeni tiwone ngati mau ake ndi oona,

tiwone zimene zidzamufikire

pakutha pa moyo wake.

18Ngati wolungamayo ndi mwanadi wa Mulungu,

Mulungu adzamuthandiza,

adzampulumutsa kwa adani ake.

19Timuyese pakumusautsa ndi kumunyoza,

kuti tiwone ngati ndi munthu wofatsa,

ngati ndi wodziŵa kupirira.

20Timpereke ku imfa yochititsa manyazi,

paja iye akuti Mulungu adzamteteza.”

Anthu osamvera Mulungu ndi olakwa kwambiri

21Anthu oipa amaganiza zimene tanenazi,

koma ndi maganizo osokera,

kuipa kwao kumangoŵachititsa khungu.

22Sadziŵa maganizo obisika a Mulungu.

Sakhulupirira malipiro a moyo wolungama.

Sazindikira konse kuti ilipodi mphotho

ya anthu oyera mtima.

23 Gen. 1.26, 27 Ndithu Mulungu adalenga anthu

kuti akhale osafa,

adaŵapanga kuti akhale chifaniziro

cha m'mene aliri Mwiniwakeyo.

24Koma imfa idaloŵa m'dziko lino lapansi

chifukwa cha dumbo la Satana.

Izi ndi zomwe anthu ogwirizana naye Satanayo adzaonadi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help