1Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu.
2Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, adatenga Yowasi, mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero adamubisa mwanayo, kubisira Ataliya, kotero kuti sadaphedwe.
3Mwanayo adakhala ndi mlezi wake zaka zisanu ndi chimodzi akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
4Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adatumiza mau kukaitana atsogoleri a asilikali olonda mfumu ndipo a alonda a nyumba yaufumu. Adabwera nawo kwa Yehoyada ku Nyumba ya Chauta. Tsono adapangana nawo chipangano ndipo adaŵalumbiritsa m'Nyumba ya Chauta. Kenaka adaŵaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja,
5naŵalamula kuti, “Zimene mudzachite ndi izi: Inu a m'chigaŵo chija choyamba, amene mukudzatumikira pa Sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde ku nyumba ya mfumu;
6gulu lachiŵiri lidzalonde pa Chipata cha Suri, gulu lachitatu lidzalonde pa chipata cha kumbuyo kwa asilikali, azilonda pa zipata zoloŵera ku Nyumba ya Chauta.
7Tsono enawo a m'zigawo ziŵiri zija odzaŵeruka ntchito pa Sabata, iwo adzalonde ku Nyumba ya Chauta, kuti aziteteza mfumu.
8Mudzazungulire mfumuyo, aliyense atatenga zida m'manja. Wina aliyense amene at ayandikire pafupi, aphedwe. Muzikhala nayo mfumu kulikonse kumene iziyenda.”
9Atsogoleriwo adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao pa Sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao kulonda pa Sabata. Onsewo adafika kwa Yehoyada wansembe uja.
10Wansembeyo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa m'Nyumba ya Chauta.
11Tsono adandanditsa asilikaliwo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi zida m'manja mwake, kuzungulira guwalo ndiponso Nyumbayo.
12Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamdzoza namlonga ufumu. Anthu adamuwombera m'manja nkunena mofuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.”
13Tsono mfumukazi Ataliya, atamva phokoso la asilikali ndi la anthu, adapita ku Nyumba ya Chauta.
142Maf. 23.3 Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake potsata mwambo wachifumu, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake, ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
15Tsono wansembe Yehoyada adalamula atsogoleri a gulu lankhondo aja kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.”
16Choncho anthuwo adamgwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pakhomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo.
Yehoyada akonza chipembedzo(2 Mbi. 23.16-21)17Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa Chauta ndi mfumu pamodzi ndi anthu ake, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta. Anthuwo adachitanso chipangano ndi mfumu,
18Choncho anthu onse a m'dzikomo adapita ku nyumba ya Baala nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenako adapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Tsono wansembe Yehoyada adaika alonda ku Nyumba ya Chauta.
19Pambuyo pake iyeyo adandanditsa atsogoleri a ankhondo, asilikali olonda mfumu, alonda a nyumba ya mfumu, ndi anthu onse a m'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nadzera ku chipata cha alonda mpaka kukafika ku nyumba ya mfumu. Pomwepo Yowasi adakhala pa mpando waufumu.
20Motero anthu am'dzikomo adakondwa. Ndipo mumzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ku nyumba ya mfumu.
21Yowasiyo anali wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.