1Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
2Atumwi khumi ndi aŵiriwo maina ao ndi aŵa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobe, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane;
3Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
4Simoni, wa m'chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.
Yesu atuma khumi ndi aŵiri aja(Mk. 6.7-13; Lk. 9.1-6)5Anthu khumi ndi aŵiri ameneŵa Yesu adaŵatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukaloŵa m'mudzi uliwonse wa Asamariya ai.
6Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika.
7Pitani, muzikalalika kuti, ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.’
8Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.
9Musatenge ndalama m'zikwama, kaya nzagolide, kaya nzasiliva, kaya nzakopala.
10 ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.
21 nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?
Woyenera kumuwopa(Lk. 12.2-7)26 Mk. 4.22; Lk. 8.17 “Choncho inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika.
27Zimene ndikukuuzirani m'chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m'manong'onong'o, inu mukazilalikire pa madenga.
28Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.
29Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa.
30Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse.
31Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Za kuvomereza Khristu pamaso pa anthu(Lk. 12.8-9)32“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba.
332Tim. 2.12Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.
Za kugaŵikana kwa anthu chifukwa cha Yesu(Lk. 12.51-53; 14.26-27)34“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo.
35Mik. 7.6Inetu paja ndidadzalekanitsa mwana wamwamuna ndi bambo wake, mwana wamkazi ndi mai wake, mkazi ndi apongozi ake aakazi,
36mwakuti adani a munthu adzakhala a m'banja mwake omwe.
37“Munthu wokonda bambo wake kapena mai wake koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Ndipo wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga.
38Mt. 16.24; Mk. 8.34; Lk. 9.23Amene sasenza mtanda wake ndi kumanditsata, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga.
39Mt. 16.25; Mk. 8.35; Lk. 9.24; 17.33; Yoh. 12.25Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga.
Wodzalandira mphotho(Mk. 9.41)40 Lk. 10.16; Yoh. 13.20; Mk. 9.37; Lk. 9.48 “Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma.
41Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
42Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.