1Ndine, Paulo, mtumwi. Adandisankha si anthu ai, koma Yesu Khristu, ndiponso Mulungu Atate amene adamuukitsa kwa akufa.
2Ineyo pamodzi ndi abale onse amene ali nane, tikulembera mipingo ya ku Galatiya.
3Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
4Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
5Ulemu ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Amen.
Uthenga Wabwino ndi umodzi wokha6Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina.
7Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu.
8Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa.
9Ndikubwereza kunena zimene tidaanenanso kale, kuti munthu aliyense akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi Uthenga Wabwino umene mudalandira uja, iyeyo akhale wotembereredwa.
10Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.
Za m'mene Paulo adasandukira mtumwi11Abale, ntakuuzani: Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika, ndi wosachokera kwa anthu.
12Sindidaulandire kwa munthu, ndipo palibenso munthu amene adandiphunzitsa Uthengawo, koma ndi Yesu Khristu yemwe amene adawuulula kwa ine.
13 Ntc. 8.3; 22.4, 5; 26.9-11 Mudamva za mayendedwe anga kale pamene ndinali m'Chiyuda. Ndinkazunza Mpingo wa Mulungu koopsa, ndipo ndinkayesetsa kuuwonongeratu.
14Ntc. 22.3Ndinkapambana anzanga ambiri a msinkhu wanga pochita zachiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa potsata miyambo ya makolo athu.
15Ntc. 9.3-6; 22.6-10; 26.13-18Koma Mulungu adandipatula ndisanabadwe, ndipo mwa kukoma mtima kwake adandiitana.
16Tsono pamene adatsimikiza zondiwululira Mwana wake, kuti choncho ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Iye kwa anthu amene sali Ayuda, sindidapite kwa munthu aliyense kuti ndikapemphe nzeru.
17Sindidapite ngakhalenso ku Yerusalemu kwa anthu amene anali atumwi kale ine ndisanakhale mtumwi. Koma ndidapita ku Arabiya kenaka nkubwereranso ku Damasiko.
18 Ntc. 9.26-30 Pambuyo pake, patapita zaka zitatu, ndidapita ku Yerusalemu kukacheza ndi Petro, ndipo ndidangokhala naye masiku khumi ndi asanu.
19Sindidaonenso mtumwi wina aliyense kupatula Yakobe yekha, mbale wa Ambuye.
20Ndikulumbira pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberanizi ndi oona, sindikunama ai.
21Pambuyo pake ndidakafika ku madera a ku Siriya ndi a ku Silisiya.
22Koma chonsecho nkuti mipingo yachikhristu ya ku Yudeya isanandiwone ndi kundidziŵa bwino.
23Inali itangomva mbiri chabe yakuti, “Munthu uja ankatizunza kaleyu, tsopano akulalika chikhulupiriro chimene kale lija ankayesetsa kuchiwononga.”
24Motero mipingoyi inkalemekeza Mulungu chifukwa cha ine.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.