Zek. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za Yoswa, mkulu wa ansembe

1 Eza. 5.2; Chiv. 12.10 Tsono m'masomphenya Chauta adandiwonetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, ataima pamaso pa mngelo wake, ku dzanja lake lamanja kutaima Satana woti amuimbe mlandu.

2Yuda 1.9 Mngelo wa Chauta uja adauza Satanayo kuti, “Chauta akudzudzule, iwe Satana! Chauta amene adasankhula Yerusalemu akudzudzule ndithu iwe! Kodi uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”

3Yoswa anali atavala zovala zalitsiro, pa nthaŵi imene adaaima pamaso pa mngelo uja.

4Tsono mngeloyo adauza anzake omperekeza kuti, “Mvuleni zovala zake zalitsirozi.” Kenaka adauza Yoswa kuti, “Ona ndakuchotsera machimo ako, tsopano ndikuveka zovala zokongola.”

5Mngelo uja adauza omperekeza aja kuti, “Mvekeni nduŵira yabwino.” Motero adamuveka nduŵira yabwino pa mutu, namuvekanso zovala zatsopano. Nthaŵiyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pomwepo.

6Mngelo wa Chauta uja adauza Yoswa kuti,

7“Zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, ‘Mukamayenda m'njira yanga, ndi kumamveradi malamulo anga, mudzalamulira m'nyumba mwanga, ndipo mudzayang'anira mabwalo anga. Tsono ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi aŵa ali panoŵa.

8Yer. 23.5; 33.15; Zek. 6.12 Tsopano imva, iwe Yoswa, mkulu wa ansembe, imvani nanunso ansembe anzakenu, amene muli chizindikiro cha zabwino zimene zidzachitike. Ndidzabwera naye mtumiki wanga wotchedwa dzina loti “Nthambi.”

9Nawutu mwala umene ndaika pamaso pa Yoswa, mwala umodzi wa mbali zisanu ndi ziŵiri. Mwiniwakene ndidzazokotapo mau, ndidzachotsa machimo a m'dziko lino pa tsiku limodzi.

10Mik. 4.4 Tsiku limenelo, nonsenu mudzaitanizana kuti mukakondwerere ufulu wanu, aliyense atakhala pa mtengo wake wa mphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Chauta Wamphamvuzonse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help