1Abale, ndifuna kuti muzindikire bwino za mphatso za Mzimu Woyera.
2Mukudziŵa kuti pamene munali akunja, anthu ankakusokezani mwa njira izi ndi izi, kukukokerani ku mafano osalankhula.
3Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti munthu amene Mzimu wa Mulungu amamtsogolera, sanganene kuti, “Yesu atembereredwe.” Ndiponso, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, “Yesu ndi Ambuye.”
4 Aro. 12.6-8 Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi.
5Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timaŵatumikira ndi amodzimodzi.
6Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense.
7Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.
8Mzimu Woyera amapatsa munthu wina mphatso ya kulankhula zanzeru, ndipo Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kulankhula mau olangiza anthu.
9Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kukhulupirira, ndipo Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amapatsa wina mphatso ya kuchiritsa matenda.
10Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo.
11Amene amachititsa anthu zonsezi ndi Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Amagaŵira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kumgaŵira.
Akhristu ali ngati ziwalo za thupi la Khristu12 Aro. 12.4, 5 Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha.
13Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
14Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri.
15Nanga phazi litanena kuti, “Poti sindine dzanja, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho?
16Nanga khutu litanena kuti, “Poti sindine diso, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho?
17Kodi thupi lonse likadakhala diso lokha, bwenzi munthu akumva bwanji? Kapena thupi lonse likadakhala khutu lokha, bwenzi munthu akununkhiza bwanji?
18Koma m'mene ziliri Mulungu adaika chiwalo chilichonse pamalo pake m'thupi, monga momwe adafunira.
19Ziwalo zonse zikadangokhala chiwalo chimodzi, sipakadakhala thupi konse.
20Komatu ziwalo nzambiri, ngakhale thupi ndi limodzi lokha.
21Motero diso silingauze dzanja kuti, “Ndilibe nawe ntchito.” Ndiponso mutu sungauze mapazi kuti, “Ndilibe nanu ntchito.”
22Kwenikwenitu ziwalo zimene zimaoneka ngati zofooka, ndizo zofunika kopambana.
23Ziwalo zimene timaziyesa zotsika, ndizo timazilemekeza kopambana. Ndipo ziwalo za thupi lathu zimene zili zochititsa manyazi, ndizo timaziveka kopambana.
24Koma zimene zili zooneka bwino, nkosafunikira kuti tiziveke motero. Mulungu polumikiza ziwalo za thupi, adazilumikiza mwa njira yoti adapereka ulemu woposa kwa ziwalo zimene zimausoŵadi ulemuwo.
25Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana.
26Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao.
27Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.
28Aef. 4.11Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
29Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa?
30Kodi onse ali ndi mphatso ya kuchiritsa matenda? Kodi onse angathe kulankhula zilankhulo zosadziŵika? Kodi onse angathe kuzitanthauzira?
31Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana.
Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni:
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.