Deut. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chizoloŵezi choletsedwa polira maliro

1 Lev. 19.28; 21.5 Inu ndinu anthu a Chauta, Mulungu wanu. Mukamalira maliro, musamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi.

2Eks. 19.5, 6; Deut. 4.20; 7.6; 26.18; Tit. 2.14; 1Pet. 2.9 Ndinu ake a Chauta, Mulungu wanu, popeza kuti wakusankhulani pakati pa anthu a pa dziko lonse lapansi, kuti mukhale anthu akeake.

Za nyama zoyenera kuzidya ndi zosayenera kuzidya(Lev. 11.1-47)

3Chilichonse chimene Chauta akuti nchonyansa, musadye.

4Nyama zoti muzidya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, mbuzi,

5ngondo, nswala, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale.

6Mungathe kudya nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogaŵikana ndiponso yobzikula.

7Koma pakati pa nyama zaziboda kapena zobzikula, musadye izi: ngamira, kalulu ndi mbira, chifukwa ngakhale zimabzikula, koma zilibe ziboda zogaŵikana.

8Nkhumbanso ndi yonyansa kwa inu. Ziboda ili nazo, komatu sibzikula. Nyama zimenezi musamadya, ndipo musamazikhudza zikafa.

9Mwa zonse zokhala m'madzi mungathe kudya izi: zonse zimene zili ndi zipsepse ndi mamba.

10Koma zonse zopanda zipsepse ndi mamba ndi zonyansa kwa inu, choncho musadye.

11Mbalame zonse zoyenera kuzidya, mudye.

12Koma mbalame zosayenera kuzidya ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba,

13kamtema, khungubwi ndi mtundu uliwonse wa mwimba,

14mtundu uliwonse wa akhungubwi,

15nthiŵatiŵa, chipudo, kakoŵa, mtundu uliwonse wa akabaŵi,

16nkhutukutu, mantchichi, tsakwe,

17vuwo, dembo, chiswankhono,

18indwa ndi chimeza ndi zina za mtundu umenewu, ndiponso nsadzu ndi mleme.

19Ziwala zonse zamapiko ndi zonyansa, choncho musadye zimenezo.

20Koma zonse zamapiko zosaipitsidwa mungathe kudya.

21 Eks. 23.19; 34.26 Nyama iliyonse yofa yokha, musadye. Alendo okha amene mumakhala nawo, alekeni adye, kapena mungogulitsa nyamayo kwa alendo ena. Pajatu inu ndinu opatulika a Chauta, Mulungu wanu. Musaphike mwanawankhosa kapena mwanawambuzi mu mkaka wa make.

Lamulo la chachikhumi

22 Lev. 27.30-33; Num. 18.21 Chachikhumi muziika padera, ndiye kuti limodzi mwa magawo khumi a zokolola zanu za chaka ndi chaka.

23Tsono pitani mukakhale pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzasankhula kuti anthu azidzampembedzerapo. Ndipo magawo achachikhumi ameneŵa mudyere pa malo amenewo, pamaso pa Mulungu wanu. Magawo ameneŵa ndi a tirigu, vinyo ndi mafuta aolivi, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a nkhosa. Muzichita zimenezi masiku onse, kuti motero muphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu.

24Koma mwina mtunda udzakutalikirani chifukwa kwatalikitsa kumalo kumene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azimpembedzerako. Motero inu mudzalephera kupita nawo kumeneko magawo anu achachikhumiwo, amene mwaŵapeza chifukwa cha madalitso a Chauta, Mulungu wanu.

25Pamenepo mugulitse zinthuzo, ndipo ndalama zake mupite nazo ku malo achipembedzowo.

26Ndalamazo mugulire zilizonse zimene mufuna, monga nyama yang'ombe, nyama yankhosa, vinyo ndiponso zakumwa zaukali, malinga nkukhosi kwanu. Tsono inuyo pamodzi ndi mabanja anu, mudzadye ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.

27Koma Alevi amene mumakhala nawo m'midzi mwanu musaŵaiwale, popeza kuti alibe dziko kapena choloŵa chaochao.

28Chaka chachitatu chilichonse muzibwera ndi magawo onse achachikhumi ochokera ku zopereka zanu za chaka chimenecho, ndi kuŵaika poyera m'midzi mwanu.

29Chakudya chimenechi ncha Alevi, poti alibe zaozao. Ndiponso ncha alendo ndi cha ana amasiye ndi akazi amasiye amene amakhala nanu pamodzi m'midzi mwanu. Anthu otere azibwera kudzatenga zimene akusoŵa. Muzichita zimenezi kuti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitseni pa ntchito zanu zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help