1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aisraele kuti pamene mwamuna kapena mkazi achita malumbiro apadera a unaziri, kuti adzipereke kwa Chauta,
3Lk. 1.15 asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Asamwe vinyo wopangidwa ndi mphesa kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo asamwe madzi amphesa kapena kudya mphesa zaziŵisi kapena zouma.
4Masiku onse pamene munthuyo ali wodzipereka kwa Chauta, asadye chilichonse chochokera ku mphesa, ngakhale mbeu zake kapena makungu ake.
5“Pa masiku onse amene adalumbira kuti adzakhala wodzipereka kwa Chauta, asamete kumutu kwake ndi lumo. Adzakhale wake wa Chauta nthaŵi zonse mpaka atatha masiku ake odzipereka kwa Chauta. Alilekerere tsitsi lake kuti likule.
6“Masiku onse pamene munthuyo wadzipereka kwa Chauta, asayandikire mtembo.
7Asadziipitse poyandikira mtembo wa bambo wake, wa mai wake, wa mbale wake kapena wa mlongo wake, chifukwa kulumbira kwa kudzipereka kwake kwa Mulungu kuli pamutu pake.
8Munthuyo ndi wopatulikira Chauta masiku onse a kudzipereka kwake.
9“Ngati munthu wina aliyense afa mwadzidzidzi pafupi naye, ndipo pakutero aipitsa tsitsi lake loperekedwalo, amete kumutu kwake pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku lomuyeretsa.
10Pa tsiku lachisanu ndi chitatu abwere ndi nkhunda ziŵiri kapena njiŵa ziŵiri kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano.
11Wansembeyo apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Tsono amchitire mwambo wopepesera machimo ake, chifukwa adalakwa poyandikana ndi mtembo. Tsiku lomwelo aperekenso tsitsi lake kwa Chauta,
12mwiniwakeyo akhale wake wa Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. Tsono abwere ndi mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti aperekere nsembe yopepesera kupalamula. Koma masiku a kudzipereka kwake koyamba kuja asaŵerengere, chifukwa kudzipereka kwakeko adakuipitsa.
13 Ntc. 21.23, 24 “Lamulo la Mnaziri pamene nthaŵi ya kudzipereka kwake yatha, nali: abwere naye pakhomo pa chihema chamsonkhano,
14ndipo iye apereke mphatso zake kwa Chauta. Apereke mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi wopanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza. Apereke nkhosa imodzi yaikazi ya chaka chimodzi yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa imodzi yamphongo yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yachiyanjano.
15Aperekenso dengu la buledi wosafufumitsa, makeke a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa topyapyala ndi topaka mafuta, pamodzi ndi zopereka zake za zakudya ndi zachakumwa.
16Tsono wansembe abwere nazo zonsezo pamaso pa Chauta. Poyamba apereke nsembe yake yopepesera machimo ndi nsembe yake yopsereza.
17Atatero, apereke nkhosa yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yachiyanjano, pamodzi ndi dengu la buledi uja wosafufumitsa. Kenaka aperekenso chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.
18Mnaziriyo amete kumutu kwake koperekedwa kuja pakhomo pa chihema chamsonkhano. Ndipo atenge tsitsi la ku mutu wake woperekedwawo, ndi kulitentha pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
19Tsono wansembe atenge mwendo wamwamba wa nkhosa yamphongo wophika, ndipo atengenso keke imodzi yosatupitsidwa, pamodzi ndi mtanda umodzi wa buledi wosatupitsidwa, ndipo aziike m'manja mwa Mnaziri, atameta tsitsi lake loperekedwa lija.
20Ndipo wansembeyo azipereke moweyula, kuti zikhale nsembe zoweyula pamaso pa Chauta. Zimenezi nzoyera, zokhalira wansembe, pamodzi ndi nganga yoperekedwa moweyula ija. Pambuyo pake Mnaziri angathe kumwa vinyo.
21“Limeneli ndilo lamulo la munthu amene alumbira kuti akhale Mnaziri. Zinthu zake zimene apereka kwa Chauta zikhale zomwe adalumbirira pa unaziri, osaŵerengera zina zimene angathe kupereka moonjezerapo. Zimene adalumbira kuti adzachita, achite momwemo potsata lamulo la kudzipereka kuti adzakhale Mnaziri.”
Za maperekedwe a madalitso22Chauta adauza Mose kuti,
23“Uza Aroni ndi ana ake
kuti azidalitsa Aisraele motere:
24Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni.
25Chauta akuyang'aneni mwachikondi
ndipo akukomereni mtima.
26Chauta akuyang'aneni mwachifundo,
ndipo akupatseni mtendere.”
27Ndipo Chauta adati, “Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzaŵadalitsadi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.