1 Maf. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyumba yachifumu ya Solomoni

1Solomoni adatha zaka khumi ndi zitatu akumanga nyumba yake yachifumu, ndipo adaimariza nyumba yonseyo.

2Nyumbayo inali ndi chigawo china chachikulu chotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. M'litali mwake inali mamita 44, m'mimba mwake inali mamita 22, msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. Adaimanga pamwamba pa mizere inai ya nsanamira zamkungudza, ndipo panali mitanda yamkungudza pamwamba pa nsanamirazo.

3Pamwamba pa mitandapo panali matabwa amkungudza okuta zipinda zimene zidaamangidwa pa nsanamira 45, pa mzere uliwonse nsanamira khumi ndi zisanu.

4Panalinso mafuremu a mawindo mizere itatu, windo kupenyana ndi windo linzake. Mawindowo ankapenyana atatuatatu.

5Ndipo makomo onse ndi mawindo omwe, mafuremu ake anali olingana monsemonse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake, ndipo windo linkapenyana ndi windo linzake pa mizere itatu.

6Panali chigawo chinanso chachikulu chotchedwa Holo ya Nsanamira. M'litali mwake inali ya mamita 22, m'mimba mwake inali ya mamita 13 ndi hafu. Patsogolo pake panali kakhonde ka nsanamira kokhala ndi denga lake.

7Adamanganso chigawo china chachikulu chotchedwa Holo ya Mpando Wachifumu, kapena Holo ya Chiweruzo, modzaweruzira milandu. M'kati mwake adaikuta ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i.

8 1Maf. 3.1 Tsono nyumba yakeyake kumene ankayenera kukakhalako, adaimanga ku bwalo lina, kumbuyo kwa holo imeneyo. Adaimanga chimodzimodzi ngati holoyo. Ndipo adamanganso chigawo china chofanana ndi holo ya Mpando wachifumu ija kumangira mkazi wake, mwana wa Farao.

9Zonsezi zidamangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene adaisema potsata miyeso yake yofunika, yochekedwa ndi sowo m'kati ndi kunja komwe. Miyala yotere adamangira nyumba kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, kuyambiranso m'bwalo la Nyumba ya Chauta mpaka ku bwalo lalikulu.

10Mazikowo adamangidwa ndi miyala yabwino kwambiri, yaikulu bwino, kutalika kwake inali mamita atatu ndi theka, ina mamita anai.

11Ndipo pamwamba pake panalinso miyala yabwino kwambiri yosemedwa potsata miyeso yake yofunika, ndiponso pamwamba pa miyalayo panali matabwa amkungudza.

12Bwalo lalikulu kuzungulira nyumbayo lidamangidwa mizere itatu yamiyala yosemedwa, ndi mzere umodzi wa mitengo yamkungudza. Bwalo lam'kati la nyumbayo ndiponso khonde lake la nyumbayo adazimanga chimodzimodzi.

Ntchito ya Huramu

13Tsono mfumu Solomoni adatumiza mau ku Tiro kukaitana Huramu kuti abwere.

14Iyeyo anali mwana wa mai wamasiye wa fuko la Nafutali, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro, mmisiri wa mkuŵa. Huramuyo anali wanzeru kwambiri, womvetsa zinthu, ndiponso waluso popanga zinthu zilizonse zamkuŵa. Adafika kwa mfumu Solomoni, nagwira ntchito zonse za Solomoniyo.

Nsanamira ziŵiri zamkuŵa

15Huramu adasungunula mkuŵa, napanga nsanamira ziŵiri. Nsanamira ina msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu, ndipo mjintchi wake unali pafupi mamita asanu ndi theka. Nsanamirayo inali ndi mphako, ndipo kuchindikira kwake kunali ngati kuyesa zala zinai. Nsanamira inzakeyo inali chimodzimodzi.

16Adasungunula mkuŵa, napanganso mitu iŵiri, ndipo adaiika pamwamba pa nsanamira zija. Mutu wina kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, ndipo winawo kutalika kwake kunalinso mamita aŵiri nkanthu.

17Ndipo adapanga maukonde aŵiri olukanalukana ndi oyangayanga, naŵaika pa mitu ya pa nsanamirazo. Ukonde umodzi pa mutu wina, ndiponso ukonde umodzi pa mutu winanso.

18Adapanganso mizere iŵiri ya zinthu zonga makangaza mozungulira pamwamba pa ukonde, kuti aphimbe mutu wa pamwamba pa nsanamira. Adachitanso chimodzimodzi ndi mutu winawo.

19Tsono mitu imene inali pamwamba pa nsanamira m'khonde, inali itasemedwa ngati maluŵa a kakombo, kutalika kwake pafupifupi mamita aŵiri.

20Mituyo inali pamwamba pa nsanamira ziŵiri zija, ndiponso pamwamba pa chigawo choulungika cha pambali pake pa ukondewo. Pa mutu umodzi panali makangaza okwanira 200 pa mizere iŵiri yozungulira, ndipo pa mutu winawo panalinso chimodzimodzi.

21Adaika nsanamirazo patsogolo pa khonde loloŵera ku Nyumba ya Chauta, ina chakumwera, imene adaitchula Yakini, ndipo ina chakumpoto, imene adaitchula Bowazi.

22Tsono pamwamba pa nsanamira zija adakongoletsapo ndi zosemasema zooneka ngati maluŵa a kakombo. Motero ntchito ya nsanamirazo idamalizika.

Thanki lamkuŵa(2 Mbi. 4.2-5)

23Pambuyo pake Huramu adapanga thanki lamkuŵa. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka.

24M'munsi mwa milomo yake adazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga.

25Adalisanjika pa ng'ombe zamkuŵa khumi ndi ziŵiri. Zitatu kuyang'ana kumpoto, zitatu kuyang'ana kuzambwe, zitatu kuyang'ana kumwera, zitatu kuvuma. Thankilo linali litakhazikika pa ng'ombezo, ndipo kuti miyendo yonse yamunsi ya ng'ombezo idaaloza cham'kati.

26Thankilo kuchindikira kwake kunali ngati chikhatho. M'milomo mwake munkaoneka ngati m'milomo mwa chikho, ngati duŵa la kakombo. Munkaloŵa madzi okwanira malita 40,000.

27Tsono adapanganso maphaka khumi amkuŵa oyenda. Phaka lililonse muutali mwake linali pafupifupi mamita aŵiri, muufupi mwake linalinso pafupifupi mamita aŵiri, ndipo msinkhu wake unali mita imodzi nkanthu.

28Maphakawo adapangidwa motere: adapangidwa ngati matabwa amkuŵa oloŵa m'mafuremu.

29Ndipo pa matabwawo panali zithunzi za mikango, ng'ombe zamphongo ndi akerubi. Tsono pa mafuremuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ng'ombe zamphongozo, adazokotapo nkhata zamaluŵa mopendeketsa.

30Kuwonjezera apo, phaka lililonse linali ndi mikombero inai yamkuŵa ndiponso mitanda yake yamkuŵanso. Ndipo pa ngodya zake zinai panali zogwiriziza mbale zosambira. Popanga zogwiriziza mbalezo, m'mbali mwake adalochamo ndi nkhata zamaluŵa.

31Kukamwa kwake kunali kozungulira ndipo kudabzola pamwamba pa phakalo masentimita 44. Kuzama kwake kunali masentimita 18. Pakamwapo panali zozokota zokometsera. Ndipo matabwa ake anali aphanthiphanthi a mbali zofanana, osati oulungika ai.

32Pansi pa matabwawo panali mikombero inai. Tsono mitanda ya mikomberoyo adapangira kumodzi ndi maphakawo. Msinkhu wa mikomberoyo unali masentimita 66.

33Mikomberoyo idapangidwa ngati mikombero ya galeta. Mitanda yake, marimu ake, sipokosi zake ndiponso mahabu ake, zonsezo adazipanga ndi mkuŵa wosungunula.

34Phaka lililonse linali ndi zigwiriro zinai, chigwiriro chimodzi pa ngodya iliyonse. Zigwirirozo zidapangidwira kumodzi ndi maphakawo.

35Pamwamba pa phaka panali mkombero, msinkhu wake masentimita 22. Tsono pamwamba pa phakalo panalinso zogwiriziza zake ndi matabwa ake, zonsezo zinali zopangidwira kumodzi ndi phakalo.

36Pamwamba pa zogwiriziza zakezo ndi matabwa akewo panali zithunzi za akerubi, mikango ndiponso mitengo ya mgwalangwa, malinga ndi m'mene unaliri mpata wokwanira chilichonse. Pozungulira adalocha ndi nkhata zamaluŵa.

37Maphaka khumi aja adaŵapanga motero. Onsewo adapangidwa mofanana, chifukwa miyeso yake inali yolingana ndipo maonekedwe ake analinso ofanana.

38 Eks. 30.17-21 Pambuyo pake adapanga mbiya zikuluzikulu khumi zamkuŵa. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi a malita 800, ndipo pakamwa pake panali pafupifupi mamita aŵiri, kuyesa modutsa. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi mbiya yake.

39Ndipo adaika maphaka motere: chakumwera kwa nyumbayo maphaka asanu, chakumpoto maphaka asanu. Ndipo adaika thanki lija kumwera chakuvuma.

40Huramu adapanganso mikhate, mafosholo ndi mabeseni. Motero Huramu adatsiriza ntchito yonse ya Nyumba ya Chauta imene ankagwirira mfumu Solomoni:

41ndiye kuti kumanga nsanamira ziŵiri zija, kupanga ziwaya zokutira nsonga za makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamirazo, ndiponso maukonde aŵiri aja ophimba ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kw makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamirazo.

42Adatsirizanso kupanga makangaza 400 a maukonde aŵiri aja, mizere iŵiri ya makangaza pa ukonde uliwonse, kuphimbira ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kwa makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamira zija.

43Ndiponso adatsiriza maphaka khumi ndi mbiya khumi zija zokhala pa maphakawo,

44thanki lija ndi ng'ombe khumi ndi ziŵiri zosanjikapo thankilo,

45ndiponso mikhate ija, mafosholo ndi mabeseni aja.

Ziŵiya zonsezi za m'Nyumba ya Chauta, zimene Huramu adapangira mfumu Solomoni, zidapangidwa ndi mkuŵa wonyezemira.

46Mfumu idapangitsa zimenezi m'chigwa cha Yordani, ku malo amtapo amene ali pakati pa Sukoti ndi Zaretani.

47Koma Solomoni adangozisiya ziŵiya zimenezo osaziyesa pa sikelo, chifukwa zidaalipo zambirimbiri. Motero kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike.

48 Eks. 30.1-3; Eks. 25.23-30 Solomoni adapangitsanso ziŵiya zimene zinali m'Nyumba ya Chauta: ndiye kuti guwa lagolide, tebulo lagolide la buledi woperekedwa kwa Mulungu,

49Eks. 25.31-40zoikaponyale za golide weniweni, kumwera zisanu, kumpoto zisanu, m'kati mwenimweni mwa malo opatulika. Adapangitsa maluŵa, nyale ndi mbano, zonse zagolide.

50Adapangitsanso zikho, zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani, ndiponso ziwaya zopalira moto, zonse za golide weniweni. Ndipo adapangitsa ndi golide zomangira zitseko za chipinda cham'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta.

51 2Sam. 8.11; 1Mbi. 18.11 Motero Mfumu Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, siliva, golide, ndi ziŵiya. Adaziika m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help