1 Mbi. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nkhondo za Davide ndi kupambana kwake(2 Sam. 8.1-18)

1Pambuyo pake, Davide adathira nkhondo Afilisti naŵagonjetsa. Ndipo adalanda Gati pamodzi ndi midzi yake yomwe kwa Afilistiwo.

2Adagonjetsanso Amowabu, ndipo Amowabuwo adasanduka otumikira Davide, ndipo ankakhoma msonkho kwa iye.

3Ku Hamati Davideyo adagonjetsanso Hadadezere mfumu ya ku Zoba, pamene inkapita kukakhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.

4Ndipo Davide adalanda Hadadezere magaleta 1,000, anthu a pa akavalo 7,000, ndi asilikali apansi 20,000. Atatero, Davide adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okoka magaleta, koma adasungako akavalo okwanira magaleta 100.

5Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000.

6Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita.

7Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu.

81Maf. 7.40-47; 2Mbi. 4.11-18Kuchokera ku Tibati ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri. Ndi mkuŵa umenewo Solomoni adapanga chimbiya ndi nsanamira ndiponso ziŵiya zina za ku Nyumba ya Chauta.

9Pamene Tou mfumu ya ku Hamati adamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse la ankhondo la Hadadezere, mfumu ya ku Zoba,

10adatuma mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Tou kaŵirikaŵiri. Tsono adamtumizira Davide mphatso zamitundumitundu zopangidwa ndi golide, siliva ndi mkuŵa.

11Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta, pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina, ndiye kuti anthu a ku Edomu, a ku Mowabu, kwa Aamoni, kwa Afilisti, ndi kwa Aamaleke.

12 Mas. 60 Pa nthaŵi imeneyi Abisai, mwana wa Zeruya, adapha Aedomu okwanira 18,000 ku chigwa cha Mchere.

13Tsono Davide adaika ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu, ndipo Aedomu onse adasanduka anthu otumikira Davideyo. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.

14Motero Davide adalamulira dziko lonse la Israele, ndipo ankayendetsa zonse mwachilungamo ndi mosakondera.

15Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri.

16Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Savisa anali mlembi.

17Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali nduna zazikulu pa ntchito zotumikira mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help