1Pambuyo pake anthu onse a ku Yuda adatenga Uziya, wa zaka 16, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake.
2Iyeyo adamanga mzinda wa Eloti naubwezera ku Yuda, mfumu itamwalira.
3Uziyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
4Adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya.
5Adadzipereka kwa Mulungu pa nthaŵi ya Zekariya amene ankamphunzitsa Uziyayo kuti azilemekeza Mulungu. Ndipo nthaŵi zonse pamene ankadzipereka kwa Chauta, Mulungu ankamupezetsa bwino.
6Nthaŵi ina Uziya adakamenyana nkhondo ndi Afilisti, nagwetsa linga la Gati ndi la Yabine ndiponso la Asidodi. Kenaka adamanga mizinda m'dziko la Asidodi ndi kwinanso m'dziko la Afilisti.
7Mulungu adamthandiza pomenyana ndi Afilisti, ndi Arabu amene ankakhala ku Guribaala, ndiponso pomenyana ndi Ameuni.
8Aamoni ankakhoma msonkho kwa Uziya, ndipo mbiri yake idamveka mpaka ku malire a Ejipito, poti anali wamphamvu kwambiri.
9Kuwonjezera pamenepo, Uziya adamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata cha ku Ndonyo, Chipata cha ku Chigwa ndi pa Mphindiko ya linga, ndipo adazilimbitsa.
10Pambuyo pake adamanga nsanja ku chipululu ndi kukumba zitsime zambiri, poti anali ndi ziŵeto zambiri ku madambo ndi ku zigwa. Analinso ndi anthu olima minda ndi anthu omasamala mphesa ku mapiri, ndiponso ku maiko achonde, poti ankakonda kulima.
11Komanso Uziyayo anali ndi gulu la asilikali odziŵa nkhondo. Anali m'magulumagulu potsata dongosolo limene adaalikonza mlembi Yeiyele ndi Maaseiya, mkulu wankhondo. Amene ankaŵalamulira asilikaliwo anali Hananiya, mmodzi mwa nduna za mfumu.
12Chiŵerengero chonse cha atsogoleri amphamvu, olimba mtima, akulu a mabanja, chinali 2,600.
13Atsogoleri ameneŵa ankalamulira gulu lankhondo lokwanira asilikali 307,500, amene ankatha kumenya nkhondo mwamphamvu, kuthandiza mfumu polimbana ndi adani.
14Ndipo adapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zisoti zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta, ndi miyala yoponyera.
15Ku Yerusalemu anthu aluso adapanga makina amene ankaŵakweza pa nsanja ndi pa malo onse andonyo, kuti anthu aziponyera mivi ndiponso miyala ikuluikulu. Choncho mbiri ya Uziya idamveka nikafika kutali, chifukwa anali atathandizidwa kodabwitsa, mpaka adakhala wamphamvu.
Uziya alakwa, nalangidwa16Koma Uziyayo mphamvu zake zitachuluka, adayamba kunyada ndipo kunyada kwakeko kudamuwonongetsa. Anali wosakhulupirika kwa Chauta Mulungu wake, ndipo adaloŵa ku Nyumba ya Chauta kuti akafukize lubani pa guwa lofukizapo lubani.
17Koma wansembe Azariya adaloŵa pambuyo pa iyeyo, pamodzi ndi ansembe a Chauta 80 olimba mtima.
18Eks. 30.7, 8; Num. 3.10 Tsono ansembewo adamletsa mfumu Uziya namuuza kuti, “Pepani, mfumu Uziya, sindinu amene muyenera kufukiza lubani kwa Chauta, koma ansembe, ana a Aaroni, amene adaŵapatula kuti azifukiza lubani. Chokaniko ku malo opatulika kwambiriŵa. Kutereku mwalakwa, ndipo ulemerero wa Chauta wakuchokerani.”
19Apo Uziya adapsa mtima. Tsono m'manja mwake munali chofukizira lubani. Ndipo atakwiyira ansembewo, khate lidatuluka pamphumi pake, ansembe aja akuwona, m'Nyumba ya Chauta, pafupi ndi guwa lofukizirapo lubani.
20Azariya mkulu wa ansembe, pamodzi ndi ansembe onse atamuyang'ana, adangoona kuti wachita khate pa mphumi. Ansembewo adamkankhira kunja mwamsanga, ndipo iye mwini wake adatuluka msangamsanga, chifukwa chakuti Chauta adaamlanga.
21Uziya adakhala wakhate mpaka pa tsiku la kufa kwake. Tsono popeza kuti anali wakhate, ankakhala m'nyumba ya yekha, chifukwa anali atachotsedwa ku Nyumba ya Chauta. Motero Yotamu mwana wake ndiye amene ankayang'anira za ku nyumba ya mfumu, namalamulira anthu am'dzikomo.
22Ntchito zonse za Uziya kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, adazilemba mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.
23Yes. 6.1Tsono Uziya adalondola makoko ake ndipo adamuika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, osati m'manda mwaomo, poti anthu ankati, “Iyeyu ndi wakhate.” Ndipo Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.