1Ine Yeremiya Chauta adandiwuza
mau onena za chilala, mau ake adati,
2“Yuda akulira,
mizinda yake ikuvutika,
anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni.
Kulira kwa anthu a mu Yerusalemu kwakula.
3Atsogoleri ao otchuka akutuma antchito
ao kuti akatunge madzi.
Apita ku zitsime,
koma osapezako madzi,
ndiye akubwerera ndi mitsuko yopanda kanthu.
Achita manyazi ndipo atha nzeru,
adziphimba kumaso.
4Pansi mpouma kotheratu,
poti kulibe mvula.
Alimi akuchita manyazi,
ndipo adziphimba kumaso.
5Mbaŵala yomwe ikusiya mwana wake wakhanda
ku thengo chifukwa choti kulibe msipu.
6Mbidzi zikuima pa zitunda zopanda kanthu,
zikupuma moti ŵefuŵefu ngati nkhandwe.
M'maso mwachita chidima,
chifukwa chosoŵa msipu.”
7Anthu akuti,
“Inu Chauta, ngakhale machimo athu
akutipalamulitsa,
komabe muchitepo kanthu kuti dzina lanu lisanyozeke.
Kusakhulupirika kwathu nkwakukuludi.
Takuchimwirani zedi.
8Inu Chauta, amene muli chikhulupiriro cha Aisraele,
ndiponso Mpulumutsi wao pa nthaŵi ya mavuto,
mukukhaliranji ngati mlendo m'dziko lino,
ngati wapaulendo wogona usiku umodzi?
9Chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru?
Mukukhaliranji ngati wankhondo amene
sangathenso kupulumutsa anthu?
Komabe Inu Chauta, muli pakati pathu,
ife amene timadziŵika ndi dzina lanu,
choncho musatisiye tokha.”
10Chauta akunena za anthu ameneŵa kuti, “Amakonda kuyendayenda kumene afuna, ndipo sangathe kudziletsa. Nchifukwa chake Ine Chauta sindingakondwere nawo, ndipo tsopano ndidzakumbukira kuipa kwao, ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.”
11Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Usaŵapempherere anthu ameneŵa, kuŵafunira zabwino.
12Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwao. Ndipo ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Koma ndidzaŵaononga ndi nkhondo, njala ndi mliri.”
13Koma ine ndidati, “Ha, Inu Chauta, aneneri ao amauza anthu kuti sadzafa ndi nkhondo, ndipo simudzagwa njala m'dziko mwathu, koma mudzakhala mtendere wokhawokha.”
14Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake.
15Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti aneneri ameneŵa akulosa m'dzina langa pamene sindidaŵatume. Amakuuzani kuti simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala m'dziko lino. Koma aneneriwo ndiwo amene adzaphedwe pa nkhondo kapena kufa ndi njala.
16Anthu amene adaŵalosera adzaponyedwa m'miseu ya mu Yerusalemu, atafa pa nkhondo kapena ndi njala. Iwowo, akazi ao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, onse adzafa, ndipo sipadzaoneka oika maliro ao. Ndithu ndidzaŵalanga poŵagwetsa m'mavuto oŵayenerera.”
17“Ukaŵauze kuti,
‘Maso anga adze misozi kosalekeza usiku ndi usana.
Pakuti anthu anga osankhidwa ali ndi bala lalikulu,
akanthidwa kwamphamvu.
18Ndikamayenda ku thengo,
ndikuwona anthu ophedwa pa nkhondo.
Ndikaloŵa mu mzinda,
ndikuwona anthu ofa ndi njala.
Aneneri ndi ansembe akupitirizabe
ntchito zao m'dzikomo,
koma osadziŵa zimene akuchita.’ ”
Anthu adandaulira Chauta19Kodi anthu a ku Yuda mwaŵatayiratu?
Kodi anthu a mu Ziyoni akuipirani m'maso?
Chifukwa chiyani mwatikantha
kotero kuti sitingathenso kukhala bwino?
Tinkayembekeza mtendere,
koma sitidaupeze.
Tinkayembekeza kuchira,
koma tidangoopsedwa kwambiri.
20Inu Chauta, tikuvomera kuipa kwathu
ndiponso kupalamula kwa makolo athu.
Ifeyo tidakuchimwiranidi.
21Musatikane, kuti dzina lanu linganyozeke.
Musanyoze mpando wanu wachifumu ndi waulemerero.
Mukumbukire chipangano chanu ndi ife,
ndipo musachiphwanye.
22Pakati pa milungu yonama ya anthu a mitundu ina,
kodi alipo mulungu wina amene angathe kupereka mvula?
Kodi mlengalenga umapereka mvula pawokha?
Kodi Inu Chauta, suja ndinu nokha
amene mumachita zimenezi?
Nchifukwa chake timakhulupirira Inu,
popeza kuti ndinu amene mumachita zinthu zonsezi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.