Zek. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mneneri aona choikaponyale chagolide

1Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabweranso nandidzutsa monga momwe amadzutsira munthu amene ali m'tulo.

2Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira.

3Chiv. 11.4Pambali pake pa choikaponyalecho pali mitengo iŵiri ya olivi, wina ku dzanja lamanja, wina ku dzanja lamanzere.”

4Ndiye mngelo amene anali naneyo ndidamufunsa kuti “Mbuye wanga, kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?”

5Mngeloyo adayankha kuti, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidati, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.”

6Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.

7Kodi iwe phiri lalitali, ndiwenso chiyani? Udzasanduka dziko losalala pamaso pa Zerubabele. Ndipo akadzabwera nawo mwala wotsiriza wa pa Nyumba yanga, namauika pamwamba, anthu adzafuula kuti, ‘Ati kukongola ati!’ ”

8Chauta adandipatsanso uthenga uwu wakuti,

9“Zerubabele adamanga maziko a nyumba imeneyi ndi manja ake, adzaitsiriza ndi manja ake omwewo. Motero anthu adzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa iwo.

10Eza. 5.2

Chiv. 5.6 Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa.

“Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.”

11Chiv. 11.4 Tsono ndidamufunsa munthuyo kuti, “Nanga mitengo iŵiri ya olivi ili kumanja ndi kumanzere kwa choikaponyalecho ikutanthauza chiyani?”

12Ndidamufunsanso kuti, “Pambali pa mipopi iŵiri yagolide yodzera mafutayo pali nthambi ziŵiri za mtengo wa olivi, zimenezi zikutanthauza chiyani?”

13Iye adati, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidayankha kuti, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.”

14Tsono iye adati, “Ameneŵa ndi anthu aŵiri odzozedwa aja, amene amatumikira Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help