1Tsono tinene chiyani za Abrahamu, kholo la ife Ayuda? Iyeyu adapezana ndi zotani?
2Chifukwa iye uja achipezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zake, bwenzi atakhala nacho chifukwa chonyadira. Koma ai, pamaso pa Mulungu sangathe kunyada.
3Gen. 15.6; Aga. 3.6 Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
4Munthu akagwira ntchito, amalandira malipiro. Malipirowo sitinena kuti ndi mphatso ai, koma timati ndi zimene munthu ayeneradi kulandira chifukwa cha ntchito zake.
5Koma munthu atangokhulupirira, m'malo mwa kudalira ntchito zake, Mulungu amene amaŵaona kuti ngosapalamula anthu ochimwa, munthu ameneyo pakukhulupirira, Mulungu adzamuwona kuti ngwolungama pamaso pake.
6Davide adaanenanso zomwezo pamene adati ngwodala munthu amene Mulungu amuwona kuti ngwolungama popanda ntchito. Paja iye adanena kuti,
7 Mas. 32.1, 2 “Ngodala anthu
amene Mulungu adaŵakhululukira machimo ao,
amene Iye adaŵafafanizira machimo ao.
8Ngwodala munthu
amene Ambuye saŵerengeranso machimo ake.”
9Kodi madalitso ameneŵa amakhalira oumbalidwa okha, kapena ndi osaumbalidwa omwe? Amakhalira ndi osaumbalidwa omwe, popeza kuti paja Malembo tatchulaŵa akunena kuti, “Abrahamu adaakhulupirira Mulungu, tsono pakukhulupirirapo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.”
10Nanga ndi liti zidachitika zimenezi? Kodi ndipo ataumbalidwa kapena asanaumbalidwe? Sizidachitike ataumbalidwa ai, koma asanaumbalidwe.
11Gen. 17.10 Kuumbalidwako kudachitika pambuyo pake, kuti chikhale ngati chizindikiro chotsimikiza kuti asanaumbalidwe, adaapezeka kale kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhululirira. Motero Abrahamu ndi kholo la onse okhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu amaŵaona kuti ngolungama, ngakhale ndi osaumbalidwa.
12Ndiponso ndi kholo la onse oumbalidwa, osati okhawo amene adangoumbalidwa m'thupi mokha, komanso amene akutsata chitsanzo cha chikhulupiriro cha kholo lathu Abrahamu asanaumbalidwe.
Abrahamu adalandira lonjezo pakukhulupirira13 Gen. 17.4-6; 22.17, 18; Aga. 3.29 Abrahamu ndi zidzukulu zake adalandira kwa Mulungu lonjezo lakuti dziko lapansi lidzakhala lao. Adalandira lonjezolo osati chifukwa cha kusunga Malamulo, koma chifukwa cha chilungamo chofumira m'chikhulupiriro.
14Aga. 3.18Ngati ndi odalira Malamulo okha amene adzalandire zimene Mulungu adalonjeza, ndiye kuti chikhulupiriro nchopanda pake, ndipo lonjezo lija lilibe phindu.
15Malamulo amangodzetsa chilango, koma kumene kulibe malamulo, kulibenso kuŵaphwanya.
16 Aga. 3.7 Nchifukwa chake lonjezolo maziko ake ndi chikhulupiriro, kuti likhale mphatso yaulere ya Mulungu, ndipo patsimikizike kuti lonjezolo adzalilandiradi anthu ofumira kwa Abrahamu. Osati okhawo amene amasunga Malamulo a Mose ai, komanso onse okhala ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu. Iye ndiyedi kholo la ife tonse.
17Gen. 17.5 Paja Malembo akuti, “Ndakuika kuti ukhale kholo la mitundu yambiri ya anthu.” Lonjezo limeneli Abrahamu adalilandira kwa Mulungu mwini amene iye ankamukhulupirira. Ndi Mulungu amene amabwezera moyo kwa akufa, ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.
18Gen. 15.5 Mulungu adati, “Zidzukulu zako zidzachulukadi.” Ndipo ngakhale zimenezi zinali zosayembekezeka konse, Abrahamu adalimbikirabe kukhulupirira kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
19Gen. 17.17 Zaka zake zinali pafupi makumi khumi, ndipo adaadziŵa kuti thupi lake linali ngati lakufa kale, ndiponso kuti Sara anali wouma.
20Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu.
21Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.
22Nchifukwa chake, monga mau a Mulungu akunena, “Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
23Mau a m'Malemboŵa onena kuti, “Mulungu adamuwona kuti ngwolungama,” sangonena za iye yekha ai.
24Akunenanso za ife amene tidzapezeka kuti ndife olungama pakukhulupirira Mulungu, amene adaukitsa Yesu Ambuye athu kwa akufa.
25Yes. 53.4, 5Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.