Mas. 61 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chitetezoKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide loimbira zipangizo zazingwe.

1Inu Mulungu, imvani kulira kwanga,

mverani pemphero langa.

2Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi,

ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu.

Munditsogolere ku thanthwe lalitali.

3Inutu ndinu kothaŵira kwanga,

nsanja yolimba yonditeteza kwa adani.

4Mundilole ndizikhala m'Nyumba mwanu nthaŵi zonse.

Mundilole ndibisale pansi pa mapiko anu

kuti munditeteze.

5Inu Mulungu, mwamva zimene ndalumbira popemphera.

Inu mwandipatsa choloŵa

chimene amalandira anthu oopa dzina lanu.

6Talikitsani moyo wa mfumu,

zaka zake zifikire ku mibadwo ndi mibadwo.

7Akhale pa mpando wake waufumu

pamaso pa Mulungu mpaka muyaya.

Inu Chauta, mumsunge mokhulupirika

chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

8Motero nthaŵi zonse

ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu,

tsiku ndi tsiku ndidzachitadi zimene ndidalumbirazo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help