1Apo Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti,
2“Kodi ndiwe amene ukusokoneza uphungu wanga
polankhula mau opanda nzeru?
3Onetsa chamuna,
ndidzakufunsa, ndipo undiyankhe.
4“Kodi udaali kuti pamene ndinkaika
maziko a dziko lapansi?
Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu.
5Nanga kodi ukudziŵa amene adalemba malire ake,
amene adayesapo ndi chingwe padzikopo?
6Kodi maziko ake adaŵakumba potani?
Nanga mwala wake wapangodya adauika ndani?
7 Bar. 3.34 Pa nthaŵiyo nyenyezi zakuvuma zinkaimba pamodzi,
ndipo angelo onse a Mulungu ankafuula mokondwa?
8 Yer. 5.22 “Kodi ndani amene adatsekera nyanja
pamene inkalengedwa
pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko?
9Ndinetu amene ndidakuta nyanjayo ndi mitambo,
ndidaiveka mdima ngati chovala.
10Ndidailembera malire,
ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake.
11Tsono ndidati, ‘Ufike mpaka apo osabzolapo,
mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.’
12“Kodi chibadwire chako udalamulapo dzuŵa
kuti lituluke m'maŵa,
ndi kuti mbandakucha ukhalepo pa nthaŵi yake?
13Kodi iweyo udalamulapo
kuti kuŵala kwa mbandakuchawo
kuunikire dziko lonse lapansi,
kuti kuthaŵitse anthu oipa obisala pamenepo?
14Chifukwa cha kuŵala kwa usana
mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino
ngati makwinya a chovala
ngati zilembo za chidindo pa mtapo.
15Kuŵala kwa dzuŵa sikuŵafika anthu oipa,
choncho sangathe kugwira ntchito zao.
16“Kodi udakayendapo pansi penipeni pa nyanja
ndi kukafika pa magwero ake?
17Kodi adakuwonetsa iwe zipata za imfa?
Kodi udaonako ku dziko la anthu akufa
kumene kuli mdima wokhawokha?
18Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziŵa?
Undiwuze tsono ngati umazidziŵa zonsezi.
19“Kodi njira yopita kumene
kumakhala kuŵala ili kuti?
Nanga mdima, kwao nkuti?
20Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwaoko zimenezi,
kodi ukuidziŵa njira yopita kwaoko?
21Makamaka ukudziŵadi ati,
poti paja nthaŵi imeneyo nkuti iweyo utabadwa,
ndipo zaka zako kuchuluka ati!
22“Kodi udaloŵamo m'nyumba zosungiramo chisanu,
kapena m'mene amasungira matalala?
23Zimenezi ndazisungira nthaŵi ya mavuto,
ndidzazitumiza nthaŵi yomenyana nkhondo.
24Kodi udapitako kumene kumatulukira dzuŵa,
kapena kumene kumachokera mphepo yakuvuma?
25“Kodi ndani amene adakonza ngalande za mvula?
Ndani adakonza njira zodzeramo mphezi?
26Ndani amagwetsa mvula pa chipululu popanda anthu,
ku dziko kumene sikukhala anthu.
27Ndani amathirira dziko louma lagwaa,
kotero kuti udzu umamerapo?
28“Kodi mvula ili ndi bambo wake?
Nanga madzi a mame adaŵabeleka ndani?
29Kodi chisanu choundana adachibala ndani?
Nanga adabereka chipale chochokera kumwamba ndani?
30Ndani amasandutsa madzi kuti alimbe ngati mwala,
pamene madzi apanyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
31 Yob. 9.9; Amo. 5.8 “Kodi Nsangwe iwe ungazimange maunyolo?
Kodi zingwe za Akamwiniatsatana iwe ungathe kuzimasula?
32Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake?
Kodi ungathe kutsogolera nyenyezi yaikulu
ya Chimbalangondo pamodzi ndi tiana take?
33Kodi malamulo a mlengalenga umaŵadziŵa?
Nanga ulamuliro wake,
kodi ungaukhazikitse pa dziko lapansi?
34“Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
kuti igwetse mvula ya chigumula?
35Kodi ungathe kutumiza zing'aning'ani kuti zing'anipe,
ndi kugwera pa malo amene iwe ukufuna?
36Ndani amene adayala mitambo bwino mu mlengalenga?
Nanga ndani adalangiza mvula kuti igwere pakutipakuti?
37Wanzeru ndani amene angathe kuŵerenga mitambo,
nanga ndani angathe kupendeketsa
mitsuko ya madzi akuthambo
38amene amasandutsa fumbi matope,
ndi kuumba zibumi?
39“Kodi iwe ungathe kuufunira chakudya mkango?
Kodi ungathe kuipatsa chakudya misona yake ija,
40pamene ili khale m'mapanga mwake,
kapena pamene ikubisala m'tchire?
41Kodi khwangwala amampatsa chakudya chake ndani,
pamene maunda ake akulirira kwa Mulungu,
namadzandira chifukwa chosoŵa chakudya?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.