1“M'mabuku timapezamo kuti ndi mneneri Yeremiya amene adaalamula anthu otengedwa ukapolo aja kuti abiseko moto wina wakuguwa, monga tasimbiramu.
2Tsono ataŵapatsa buku la Malamulo, adaŵalangiza anthuwo kuti asaiŵale Malamulo a Ambuye, ndipo asasokere m'maganizo ao poona mafano agolide ndi asiliva ndi zovala zakaso zimene akunja amaŵaveka.
3Adaonjezapo malangizo ena onga omwewo akuti asalole kuti Malamulowo achoke m'mitima mwao.
4“M'mabuku omwewo, tidaŵerengamo kuti mneneriyo, Mulungu atamlamula, adatenga chihema ndi bokosi lachipangano, nakwera nazo kuphiri kumene Mose adaaonera dziko limene Mulungu adaŵapatsa.
5Atafikako, Yeremiya adapeza phanga, naikamo hema lija ndi bokosi lachipangano, ndiponso guwa lofukizirapo lubani, nkutseka pakhomo pake.
6Pambuyo pake omutsatira adabwera kuti adzalembe zizindikiro pa njira, koma njirayo sadathenso kuipeza.
7Yeremiya atazimva, adaŵadzudzula, adati, ‘Maloŵa adzakhala obisika mpaka nthaŵi imene Mulungu adzasonkhanitsenso anthu ake, ndi kuwonetsa chifundo chake.
8Eks. 16.10; 24.16; 1Maf. 8.10, 11Nthaŵi imeneyo Ambuye adzaziwonetsanso poyera zinthuzo. Ulemerero wa Ambuye ndi mtambo uja zidzaoneka, monga momwe zidaachitikira nthaŵi ya Mose ndiponso pamene Solomoni adaapemphera kuti Nyumba ya Mulungu ipatulidwe mwaulemerero.’
9“M'mabukumonso ankasimba kuti Solomoniyo, poti anali ndi luntha, adapereka nsembe yopatulira Nyumba ya Mulungu atatsiriza kuimanga.
10Ndipo monga pamene Mose adaati atapemphera kwa Ambuye, moto udatsika kumwamba nkupsereza nsembe, choncho Solomoni atapemphera, moto udatsikanso nkupsereza nsembe.
11Mose adaati, ‘Nsembe zidapserera zathunthu, chifukwa nsembe zopepesera machimo sadazidye.’
12Solomoni adachita chikondwerero cha mtundu womwewu masiku asanu ndi atatu.
13“M'mabuku ndi m'makalata onena za Nehemiya timapezamonso nkhani zina zonga zomwezi. M'menemo timaona kuti Nehemiya adamanga nyumba yosungiramo mabuku, nasonkhanitsanso mabuku okamba za mafumu ndi aneneri, ndiponso zolemba za Davide ndi makalata a mafumu onena za zopereka zaufulu.
14Chimodzimodzi Yudasinso naye adasonkhanitsa mabuku onse amene adaatayika pa nthaŵi ya nkhondo. Mabukuwo tikali nawobe m'manja mwathu.
15Tsono mukaŵafuna mabukuwo, mutume amithenga adzakutengereni.
16 1Am. 4.59 “Choncho takulemberani, chifukwa tili pafupi kuchita chikondwerero cha kuyeretsa Nyumba ya Mulungu. Mudzachita bwino kumakumbukira masiku ameneŵa.
17Mulungu ndiye adapulumutsa anthu ake onse, ndipo onse adaŵabwezera dziko lao, ufumu, unsembe ndi kupatulika kwao,
18monga adaalonjezera m'Malamulo. Motero ife tikukhulupirira kuti Iye yemwe adzatichitira chifundo posachedwa, ndipo adzatisonkhanitsanso tonsefe ku Nyumba yake yopatulika, kuchokera ku maiko onse a dziko lapansi, chifukwa adatipulumutsa ku zoipa zazikulu, ndipo adayeretsa Nyumba yake.”
Mau oyamba a mlembi19Yasoni wa ku Kirene adalemba mabuku asanu ofotokoza za mbiri ya Yudasi Makabeo ndi abale ake, za kuyeretsa Nyumba yaikulu ya Mulungu ndi za kupereka guwa lake lansembe kwa Mulungu.
20Adafotokoza za nkhondo zimene adamenyana ndi Antioko Epifane ndi mwana wake Eupatore.
21Adafotokozanso za zakumwamba zimene zidaŵaonekera amene adaalimbikira kuteteza Chiyuda. Motero, ngakhale anthuwo anali oŵerengeka, adalandanso dziko lao lonse, nathaŵitsa magulu a akunja.
22Adalandanso Nyumba ya Mulungu, yotchuka m'dziko lonse la pansi pano. Adapulumutsa mzinda, nakhazikitsanso malamulo amene anali pafupi kuiŵalika. Zonsezi adazichita chifukwa chakuti Ambuye adaaŵamvera chifundo ndi kuŵakomera mtima.
23Zonse zimene Yasoni wa ku Kirene adazifotokoza m'mabuku asanu, ife tiyesetsa kuzilemba mwachidule m'buku limodzi lokha.
24Poona kuchuluka kwa manambala amene anali m'mabukumo tidazindikira kuti wofuna kuzimvetsa bwino nkhani zakalezo, amavutika nkuchuluka kwa nkhanizo.
25Nchifukwa chake tidayesetsa kukondweretsa anthu okonda kuŵerenga, tidayesa kuŵachepetsera ntchito ofuna kuziloŵeza pamtima kuti azikumbukire, ndipo tidafuna kupindulitsa aliyense woziŵerenga.
26Ife amene tidayamba ntchito yolemba zonsezo mwachidule, tidapeza kuti si ntchito yapafupi, koma yokhetsa thukuta ndi yochezeretsa usiku.
27Zili ngati munthu wofuna kukonzera ena phwando. Iye uja amakhala ndi ntchito yolemetsa kuti akondweretse enawo. Komabe pofuna kukondweretsa aŵerengi ambiri tikuivomera ntchito yoŵaŵayo.
28Tingokhulupirira kuti amene adalemba zakalezo, adafufuza bwino zinthu zonse. Ife tingofuna kunena zomwezo mwachidule.
29Munthu womanga nyumba yatsopano amasamala za kamangidwe ka nyumba yathunthu, koma wofuna kukometsa nyumbayo ndi kuzokotamo zithunzi, amangosamala za kukometsako. Ifenso ndi momwemo.
30Kufufuza zakale, ndi kuzifotokoza pokhudza mbali zonse, ndiponso kusamala zonse ngakhale ndi zazing'ono zomwe, kumakhalira munthu amene adalemba mbiriyo pachiyambi pomwe.
31Koma wongolemba zomwezo mofuna kuzifupikitsa chabe, ayenera kuloledwa kuzinena mwachidule, osafotokoza zonse za mbiri yakale mwatsatanetsatane.
32Tiyambe tsono nkhani yathu, osaonjeza mau ena. Kukadakhala kupusa kuchulukitsa mau oyambira a mbiri yakaleyo, kwinaku nkuchepetsa mau ofotokoza za mbiri yeniyeniyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.