1Nthaŵi ina Satana adafuna kuvutitsa Aisraele, nanyenga Davide kuti aŵerenge Aisraele.
2Choncho Davide adauza Yowabu mtsogoleri wa ankhondo kuti, “Pita, ukaŵerenge Aisraele kuyambira ku Beereseba mpaka ku Dani, ndipo udzandiwuze, kuti ndidziŵe chiŵerengero chao.”
3Koma Yowabu adati, “Chauta achulukitse pa chiwerengero anthu ake makumi khumi kupambana m'mene alirimu. Kodi anthu onseŵa mbuyanga mfumu si atumiki anu? Nanga chifukwa chiyani mbuyanga akufuna zimenezi? Chifukwa chiyani akufuna kuchimwitsa Aisraele?”
4Koma mfumu idamkakamiza Yowabuyo. Motero Yowabu adachoka nayendera dziko lonse la Israele, pambuyo pake anabwerera ku Yerusalemu.
5Adapereka chiŵerengero cha anthu onse kwa Davide. Ku dziko lonse la Israele kunali anthu 1,100,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kunali 470,000 otha kumenya nkhondo.
6Koma Yowabuyo sadaphatikizepo dera la Levi ndi la Benjamini poŵerengapo, poti lamulo la mfumulo lidaamuipira.
7Mulungu nayenso sadakondwere nako kuŵerengako, choncho adaŵakantha Aisraelewo.
8Pamenepo Davide adayamba kupemphera kwa Mulungu, adati, “Ndachimwa kwambiri ine pazimene ndachitazi. Koma tsopano ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri.”
9Tsono Chauta adauza Gadi, mneneri wa Davide, kuti,
10“Pita ukamuuze Davide kuti, Ine Chauta ndikunena kuti, ‘Ndikuika pamaso pako zinthu zitatu zoti ndikuchite. Tsono usankhepo chimodzi ndipo ndidzakuchita.’ ”
11Gadi adapita kwa Davide nakamuuza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Musankhepo chimene mukufuna:
12kodi pabwere zaka zitatu za njala, kapena inu mukhale miyezi itatu akukukanthani adani anu namakukugonjetsani pa nkhondo, kapena pagwe mliri wa masiku atatu m'dzikomo pamene Chauta adzakukanthani ndi lupanga, ndipo mngelo wa Chauta adzawononga zinthu m'dziko lonse la Israele.’ Tsono tsimikizani choti ndikamuyankhe amene adanditumayo.”
13Apo Davide adauza Gadi kuti, “Ine pamenepa ine ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka ndigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde ndisagwe m'manja mwa anthu ayi.”
14Motero Chauta adatumiza mliri pa Aisraele, mwakuti adafapo Aisraele okwanira 70,000.
15Ndipo Mulungu adamtumadi mngelo uja kukaononga Yerusalemu. Koma pamene ankati aziwononga kumene, Chauta adaona namva chisoni, osafunanso kuchita choipacho. Choncho adauza mngelo woonongayo kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira, bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chauta uja ataima pa malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi.
16Davide adakweza maso ake naona mngelo wa Chautayo ataimirira pakati pa dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, m'manja mwake ali ndi lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Tsono Davide, pamodzi ndi akuluakulu omwe, atavala ziguduli, adadzigwetsa choŵerama pansi.
17Ndipo Davide adalankhula ndi Mulungu nati, “Kodi sindine amene ndidalamula kuti akaŵerenge anthu? Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi, kodi zachita chiyani? Inu Chauta Mulungu wanga, dzanja lanu likanthe ine pamodzi ndi banja la bambo wanga. Koma lisati likanthe anthu anuŵa.”
18Apo mngelo wa Chauta adalamula Gadi kuti, “Kauze Davide kuti akamangire Chauta guwa pa malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi uja.”
19Motero Davide adapita, atamva mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa Gadi.
20M'menemo nkuti Orinani akupuntha tirigu. Atacheuka adaona mngeloyo, koma ana ake aamuna anai amene anali naye, adaabisala.
21Pamene Davide adafika kwa Orinani, Orinaniyo adayang'ana, naona Davide, ndipo adatuluka ku malo opunthira tiriguko, nalambira Davide moŵeramitsa nkhope pansi.
22Davide adauza Orinani kuti, “Undipatse malo opunthira tiriguŵa, kuti ndimangirepo Chauta guwa, kuti mliriwu uŵachoke anthu. Undigulitse pa mtengo wake ndithu.”
23Tsono Orinani adauza Davide kuti, “Iyai, ingotengani, ndipo mbuyanga mfumu achite zimene zimkomere. Ndikupereka ng'ombe kuti zikhale nsembe yopsereza, mitengo yopunthira kuti ikhale nkhuni, ndiponso tirigu kuti akhale chopereka cha chakudya. Zonsezi ndikuzipereka.”
24Koma mfumu Davide adauza Orinani kuti, “Iyai, koma ndichita chogula ndi ndalama ndithu pa mtengo wake wathunthu. Sindingatenge chinthu chako kuti ndichipereke kwa Chauta, kupereka ngati nsembe yopsereza chinthu chimene sindidachigule.”
25Motero Davide adalipira Orinani masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo.
26Ndipo adamangira Chauta guwa kumeneko, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Adatama Chauta mopemba, ndipo Chautayo adamuyankha potumiza moto wakumwamba, nugwera pa guwa la nsembe zopsereza.
27Tsono Chauta adalamula mngelo wake, iye nabwezera lupanga m'chimake.
28Nthaŵi imeneyo Davide ataona kuti Chauta wamuyankha ku malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi uja, adapereka nsembe zake kumeneko.
29Chihema cha Chauta chimene adachipanga Mose kuchipululu kuja ndiponso guwa la nsembe zopsereza, zonsezo zinali ku kachisi wa ku Gibiyoni pa nthaŵi imeneyo.
30Koma Davide sadathe kupitako kukapempha nzeru kwa Mulungu, poti ankachita mantha ndi lupanga la mngelo wa Chauta uja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.