Yud. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero la Yuditi

1Tsono Yuditi adadzigwetsa choŵerama pansi, nadzola phulusa kumutu, ndipo adavula nsalu imene idaaphimba chiguduli chimene ankavala. Ndipo pa nthaŵi yamadzulo pamene anthu ankapereka lubani wofukiza m'Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, iye adayamba kupemphera kwa Ambuye mokweza mau, adati,

2Gen. 34.1-31“Inu Ambuye, Mulungu wa kholo langa Simeoni, mudampatsa lupanga kuti alipsirire alendo aja amene adavula namwali kuti amuipitse, namchititsa manyazi poonetsa ntchafu yake, kenaka nkumchita chigololo. Inu mudaanena kuti, ‘Zimenezi zisachitike,’ komabe iwo adazichita.

3Motero mudapereka atsogoleri ao kuti aphedwe pabedi pomwe ankachitira chigololo ndi mtsikanapo. Mudaŵakantha onse, akapolo, ndi mafumu ndi olamulira omwe pa mipando yao.

4Mudapereka akazi ao kuti agwidwe, ndiponso ana ao aakazi kuti atengedwe ukapolo. Mudafunanso kuti chuma chao chonse chigaŵidwe pakati pa ana anu okondedwa amene anali ndi changu chochita zimene Inu mufuna. Iwo adanyansidwa nako kuipitsidwa kwa mlongo wao, nakupemphani kuti muŵathandize. Inu Mulungu wanga, imvani pemphero langanso, ine mkazi wamasiye.

5“Pajatu ndinu amene mudachita zimene zidachitika nthaŵi imeneyo, ndi zimene zidaachitika kale ndiponso pambuyo pake. Zinthu zimene zilipo tsopano, ndi zimene zidzachitike, ndinu mudazikonzeratu. Zimene mudazikonza zidachitikadi.

6Zinthu zimene mudazifuna zidaoneka poyera ndi kunena kuti, ‘Tili pano.’ Paja Inu mumadziŵiratu zonse zimene muti muchite, ndipo mumazilamula mutaziganiziratu bwino.

7“Tsopano Aasiriya ali ndi mphamvu kupambana kale. Amanyadira ankhondo ao okwera pa akavalo ndi oyenda pansi. Amadalira mikondo yao, zishango zao, mauta ao ndi zida zoponyera miyala, koma sadziŵa kuti Inu Ambuye ndinu ngwazi yothetsa nkhondo.

8Dzina lanu ndinu Ambuye. Ndi mphamvu zanu muthetse ukali wao, ndipo mu ukali wanu muthyole magulu ao ankhondo. Pajatu iwo akonzekera kudzaononga Nyumba yanu, kudzaipitsa malo omveketsa dzina lanu lolemekezeka, ndipo kudzagwetsa ndi lupanga nyanga za guwa lanu lansembe.

9Penyani chipongwe chao, agwetsereni mkwiyo wanu, ndipo ineyo mkazi wamasiyene mundipatse mphamvu, kuti ndichite zimene ndikukonzekera.

10Mugwiritse ntchito mau anga onyenga kuti onse muŵaononge, kapolo ndi karonga ndi mtumiki wake. Kunyada kwaoko mukuwononge ndi dzanja la munthu wamkazi.

11“Mphamvu zanu zaufumu sizidalira kuchuluka kwa ankhondo kapena mphamvu zao. Inu ndinu Mulungu amene mumasamala odzichepetsa, ndinu mthandizi wa amphaŵi. Mumatchinjiriza ofooka ndi kuteteza amene ali okha. Mumapulumutsa otaya mtima.

12Imvani pemphero langa, Inu Mulungu wa kholo langa Simeoni, Mulungu amene Aisraele amamkhulupirira, wolamulira dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Inu Mlengi wolenga mitsinje ndi nyanja, mfumu ya zonse, imvani pemphero langa.

13Lolani kuti mau anga onyenga aŵapweteke adaniŵa ndi kuŵapha, chifukwa iwoŵa akonza zoipa zoti achichite chipangano chanu, Nyumba yanu yoyera, phiri la Ziyoni ndi dziko la anthu anu.

14Mtundu uliwonse wa anthu ndi fuko lililonse, onsewo akudziŵeni kuti ndinu Mulungu, Mphambe wamphamvuzonse, ndipo kuti Inu nokha ndinu amene mumatchinjiriza Israele.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help