Lev. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malamulo a nthenda zapakhungu

1Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

2“Munthu akakhala ndi chithupsa pathupi pake, kapena m'buko, kapena chikanga, ndipo mwina nkusanduka ngati nthenda ya khate pakhungu pakepo, munthuyo abwere naye kwa wansembe Aroni kapena kwa aliyense mwa ana ake amene ali ansembe.

3Wansembe aonetsetse pakhungu pali nthendapo. Akapeza kuti ubweya wa pamalo pali nthendapo wasanduka woyera, ndipo kuti nthendayo yazama ndithu kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe atamuwonetsetsa ndithu, amutchule kuti ndi woipitsidwa.

4Koma pakhungupo pakamaoneka kuti mpoyera, ndipo nthendayo sidapitirire khungu, ndipo ubweya wapamalopo sudasanduke woyera, wansembeyo amuike padera munthu wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.

5Wansembe amuwonetsetse wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Akaiwona nthendayo kuti sidafalikire pa khungu, pamenepo wansembeyo amtsekere munthu uja masiku asanu ndi aŵiri ena.

6Tsono wansembe uja amuwonetsetsenso wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Pakhungu pakakhala pothimbirira, nthendayo yosafalikira pakhungupo, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi wosaipitsidwa. Umenewo ndi m'buko chabe, tsono wodwalayo achape zovala zake, ndipo adzakhala woyeretsedwa.

7Koma m'bukowo ukafalikira pa khungu, munthuyo atadziwonetsa kale kwa wansembe kuti amuyeretse, munthuyo akaonekerenso pamaso pa wansembe.

8Wansembe amuwonetsetsenso munthuyo. Akaona kuti m'bukowo wafalikiradi pa khungu, atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa, limenelo ndi khate.

9“Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, abwere naye kwa wansembe.

10Wansembe amuwonetsetse. Akakhala ndi chithupsa cha maonekedwe oyera pa khungu, chimene chasandutsa ubweya wapamalopo kukhala woyera, ndipo pachithupsapo pakakhala zilonda,

11limenelo ndi khate lachikhalire limene lili pakhungu pakelo, ndipo wansembe amutchule kuti ndi woipitsidwa. Sikufunika kumtsekera chifukwa ndi woipitsidwadi.

12Khatelo likafalikira pa khungu, kotero kuti likhala litagwira khungu lonse la munthu wodwalayo kuyambira kumutu mpaka kumapazi, monga m'mene wansembe angaonere,

13pamenepo wansembeyo aonetsetse. Khatelo likakhala litagwira thupi lonse, wodwalayo amutchule kuti ndi wosaipitsidwa. Thupi lonse lasanduka loyera ndipo munthuyo ndi wosaipitsidwa.

14Koma pathupi pake pakaoneka zilonda, ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa.

15Tsono wansembe aonetsetse zilondazo, ndipo munthu wodwalayo amtchule kuti ndi woipitsidwa. Zilondazo nzoipitsa poti limenelo ndi khate.

16Koma zilondazo zikasinthikanso ndi kusanduka zoyera, pamenepo munthu wodwalayo abwere kwa wansembe.

17Tsono wansembeyo amuwonetsetse. Zilondazo zikakhala kuti zasanduka zoyera, wansembeyo amutchule munthu wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Ndi woyera ameneyo.

18“Pa khungu la munthu wodwalayo pakakhala chithupsa choti chidapola,

19ndipo pamene panali chithupsacho pakatuluka zotupatupa zoyera kapena banga loyera mofiirira, aziwonetse kwa wansembe.

20Wansembe aonetsetse bwino, ndipo chithupsacho chikazama, ubweya wake nusanduka woyera, wansembeyo amutchule munthu wodwala uja kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yaphulika pachithupsapo.

21Koma wansembe akaonetsetsa, napeza kuti ubweya wake sudasanduke woyera, ndipo chithupsacho sichidazame, koma chikuzimirira, wansembeyo amuike padera wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.

22Nthendayo ikafalikira pa khungu, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa, limenelo ndi khate.

23Koma bangalo likakhala pa malo amodzi, osafalikira, chimenecho nchipsera cha chithupsa. Wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa.

24“Munthu akakhala ndi bala lamoto, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera kumene,

25wansembe aliwonetsetse. Ubweya wapabangapo ukasanduka woyera, ndipo balalo likaoneka kuti lazama, limenelo ndi khate lomwe laphulika pa balalo. Wansembe atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate.

26Koma wansembe akaonetsetsa, napeza kuti ubweya wake sudasanduke woyera, ndipo balalo silidazame, koma likuzimirira, wansembe amuike padera wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.

27Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate.

28Koma bangalo likakhala pa malo amodzi losafalikira pa khungu, ndipo likuzimirira, limenelo ndi thuza la balalo. Wansembeyo amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa, popeza kuti nchipsera cha bala lamoto chabe.

29“Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena kundevu,

30wansembe aiwonetsetse nthendayo. Ikaoneka kuti ikuzama, ndipo ubweya ukakhala wachikasu ndi wotetemera, wansembeyo amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi mfundu yonyerenyesa, khate lakumutu kapenanso lakundevu.

31Wansembe ataiwonetsetsa mfundu yonyerenyesayo, niwoneka kuti sidazame, ndipo palibe ubweya wakuda pamalopo, wansembeyo amuike padera munthu wodwala mfundu yonyerenyesayo masiku asanu ndi aŵiri.

32Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonenso nthendayo. Mfunduyo ikakhala yakuti sidafalikire, ndipo palibe ubweya wachikasu, ndipo mfunduyo ikaoneka kuti sidazame,

33wodwalayo amete, koma mfunduyo asaimete. Wansembe amtsekere masiku asanu ndi aŵiri ena munthu wodwala mfundu yonyerenyesayo.

34Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonetsetsenso mfunduyo, ndipo ikakhala yakuti sidafalikire pa khungu, ndiponso ikaoneka kuti sidazame, wansembe atchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Tsono wadwalayo achape zovala zake, ndipo akhale wosaipitsidwa.

35Koma mfunduyo ikafalikira pa khungu, wodwalayo atayeretsedwa kale,

36pamenepo wansembe amuwonetsetse wodwalayo. Mfunduyo ikakhala itafalikira pa khungu, wansembe asafunefune ubweya wachikasu ai, munthuyo ndi woipitsidwa.

37Koma wansembe akaipenyetsetsa mfunduyo napeza kuti pamera ubweya wakuda, ndiye kuti mfunduyo ndi yopola. Tsono wansembe amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa.

38“Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi maŵanga oyera pa khungu,

39wansembe aonetsetse bwino. Maŵanga apakhunguwo akakhala oyerera, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pakhungupo. Tsono munthuyo ndi wosaipitsidwa.

40“Tsitsi la munthu likatha kumutu chapankhongo, ndiye kuti ndi dazi limenelo, koma munthuyo ndi wosaipitsidwa.

41Munthu akakhala wopanda tsitsi pa mphumi ndiponso m'litsipa, ndiye kuti ali ndi dazi lapamphumi, koma ndi wosaipitsidwa.

42Koma pa dazi lapankhongo kapena lapamphumi pakakhala banga la nthenda loyera mofiirira, limenelo ndi khate limene likutuluka pa nkhongo kapena pa mphumi.

43Tsono wansembe amuwonetsetse wodwalayo, ndipo banga lotupalo likakhala loyera mofiirira pa dazi lapankhongolo kapena lapamphumilo, monga m'mene limaonekera khate pa khungu,

44ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Wansembe ayenera kumtchula kuti ndi woipitsidwa, ali ndi khate lakumutu.

45“Munthu wakhate avale nsanza, ndipo tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wam'mwamba, ndipo azifuula kuti, ‘Ndine woipitsidwa, ndine woipitsidwa.’

46Wodwalayo adzakhalabe woipitsidwa nthaŵi zonse pamene ali ndi nthendayo, ndipo akhale payekha kunja kwa mahema.

Nguwi ya pa zovala

47“Chovala chaubweya kapena chathonje chikakhala ndi nguwi

48kapena nsalu yathonje kapena yaubweya, kapenanso chikopa kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa,

49ndipo nguwiyo ikakhala ndi maonekedwe achisipu kapena ofiira pa chovalapo, kapena pa thonje loluka, kapena pa chikopa, kaya pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nguwi ndithu, ndipo chovalacho achiwonetse kwa wansembe.

50Wansembeyo aiwonetsetse nguwiyo. Chovalacho achiike padera masiku asanu ndi aŵiri.

51Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri aiwonetsetsenso nguwiyo. Ikakhala itafalikira pa chovalacho, kapena pa chikopa cha ntchito ya mtundu uliwonse, imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chovalacho ndi choipitsidwa.

52Tsono wansembe achitenthe chovalacho, chifukwa nguwiyo yaipitsa chovala chaubweya kapena chathonjecho, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, poti imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chinthucho achitenthe.

53“Wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo sidafalikire pa chovalacho, kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa,

54wansembeyo alamule kuti achape chovalacho, ndipo achiike padera masiku asanu ndi aŵiri ena.

55Ndipo wansembe achiwonetsetse chovala chimenecho chitachapidwa. Ngati banga la nguwiyo silidasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti siidafalikire, chovalacho nchoipitsidwa ndithu. Muchitenthe, osasamala zakuti banga la nguwiyo lili kumbuyo kapena kumaso.

56“Koma wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo njothimbirira atachapa chovalacho, ang'ambe banga la nguwilo pa chovala chathonjecho kapena chachikopacho.

57Bangalo likaonekanso pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Zonse zanguwizo muzitenthe.

58Koma chovala, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachapa, tsono nguwiyo nkuchoka, muchapenso kachiŵiri, ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”

59Limeneli ndi lamulo la nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena m'chovala chathonje, kapenanso m'chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help