Deut. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tiyese kuti anthu aŵiri akangana. Tsono atapita ku bwalo lamilandu, aweruzi nkugamula kuti uyu sadalakwe koma wolakwa ndi winayu.

2Ngati wolakwayo ayenera kukwapulidwa, muweruziyo amlamule kuti agone pansi ndipo akwapulidwe mikwapulo yolingana ndi kulakwa kwake.

32Ako. 11.24 Angathe kumkwapula mpaka mikwapulo makumi anai, koma osapitirira pamenepo. Zikapitirira pamenepo, ndiye kuti zidzamchititsa manyazi mbale wanuyo.

4 1Ako. 9.9; 1Tim. 5.18 Ng'ombe imene ikupuntha tirigu, musaimange pakamwa.

Zoyenera kuchita wachibale akamwalira

5 Mt. 22.24; Mk. 12.19; Lk. 20.28 Abale aŵiri akamakhala pamodzi, ndipo wina nkumwalira, koma osasiya mwana, mkazi wamasiyeyo asakwatiwe ndi munthu wa banja lina. Mbale wake wa malemuyo amtenge, amkwatire ndipo apitirize ntchito ya mbale wake kwa mkazi ameneyo.

6Mwana woyamba kubadwa m'nyumbamo, adzakhala mwana wa mbale wake womwalirayo, kuti dzina la banja lake lisaferetu m'dziko la Israele.

7Rut. 4.7, 8 Koma ngati mbale wa malemuyo samufuna mkazi wa mbale wakeyo, mkaziyo angathe kupita ku chipata kwa akuluakulu ndi kukadandaula kuti, “mbale wa mwamuna wanga uja sakufuna kuti dzina la mbale wakeyo lipitirire m'dziko la Israele. Akukana kundiloŵa chokolo.”

8Pamenepo akuluakulu amumzindamo amuitane kuti alankhule naye. Akapitirira ndithu kukana kumkwatira,

9mkaziyo apite kwa mlamu wakeyo pamaso pa akuluakulu onsewo, ndipo amuvule nsapato yakumodzi, amthire malovu kumaso ndi kunena kuti, “Zimenezi ndiye zoyenera kumchitikira munthu wokana chokolo cha mbale wake.”

10M'dziko la Israele, banja la mwamunayo lidzatchedwa banja la munthu amene adamuvula nsapato yakumodzi.

Malamulo ena

11Anthu aŵiri akamamenyana ndipo mkazi wa mmodzi pofuna kupulumutsa mwamuna wake, agwira mdani wakeyo ku moyo,

12musamchitire chifundo mkazi ameneyo, mumdule dzanja.

13 Lev. 19.35, 36 Miyeso yopimira kulemera musakhale nayo iŵiri m'thumba mwanu, waukulu ndi waung'ono.

14Miyeso yopimira kuchuluka musakhale nayo iŵiri m'nyumba mwanu, waukulu ndi waung'ono.

15Miyeso ikhale miyeso yeniyeni yabwino, kuti mukakhale nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.

16Chauta amadana ndi anthu onyenga mwa njira yotereyi.

17 Eks. 17.8-14; 1Sam. 15.2-9 Kumbukirani zimene adakuchitani Aamaleke nthaŵi ija munkachoka ku Ejipitoyi.

18Analibe mantha ndi Mulungu. Motero adakuthirani nkhondo pa njira, pamene mudaali mutatheratu nkutopa. Paja adaŵapheratu anzanu onse amene ankachedwa ndi kuyenda m'mbuyo.

19Motero tsono, Chauta, Mulungu wanu, akadzakupatsani dziko kuti likhale choloŵa chanu, nadzakulanditsani m'manja mwa adani anu onse okuzungulirani, kasamaleni kuti mukaphe Aamaleke onse, kuti munthu asadzaŵakumbukenso mpang'ono pomwe. Musaiŵale zimenezi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help