1Chauta, Mulungu wanga, ndikuthaŵira kwa Inu.
Mundilanditse kwa onse ondithamangitsa.
Mundipulumutse,
2kuti iwo anganding'ambe ngati mkango,
ndi kundikadzula popanda wina wondipulumutsa.
3Chauta Mulungu wanga, ngati ndachita izi:
kumchimwira munthu aliyense,
4kubwezera choipa bwenzi langa,
kapena kumulanda zinthu mdani wanga popanda chifukwa,
5mdaniyo andithamangitse ndi kundigwira,
andipondereze pansi ndi kundipha,
andisiye ndili thasa m'fumbi.
6Nyamukani, Inu Chauta, muli okwiya,
mulimbane ndi adani anga aukali.
Dzambatukani, Inu Mulungu wanga,
amene mwalamula kuti chilungamo chichitike.
7Musonkhanitse anthu a mitundu yonse pafupi ndi Inu,
ndipo muŵaweruze mutakhala pa mpando wanu kumwamba.
8Chauta amagamula milandu ya anthu.
Tsono thetsani mlandu, Inu Chauta, moyenera,
popeza kuti ine sindidalakwe konse.
9 Chiv. 2.23 Thetsani ntchito zoipa za anthu ochimwa,
koma anthu ochita zabwino muŵabwezere zokoma.
Inu ndinu amene mumayesa maganizo ndi mitima yomwe,
Inu ndinu Mulungu wolungama.
10Mulungu ndiye chishango changa,
amapulumutsa anthu olungama mtima.
11Mulungu ndiye muweruzi wolungama,
amalanga anthu oipa nthaŵi zonse.
12Ngati munthu salapa,
Mulungu adzanola lupanga lake,
adzakunga ndi kukoka uta wake.
13Wakonza zida zake zoopsa,
waika mivi yamoto ku uta wake.
14Zoonadi, munthu woipa
amalingalira zoipa zokhazokha nthaŵi zonse,
ntchito yake ndi kunyenga
ndi kuvutitsa anthu ena basi.
15Amakumba mbuna kuti ikhale yozama,
koma amagwamo ndiye yemwe.
16Choipa chitsata mwini,
chiwawa chimabwerera pa mwini wake.
17Ine ndidzathokoza Chauta
chifukwa cha kulungama kwake,
ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Chauta,
Wopambanazonse uja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.